Prophet Shepherd Bushiri yemwe ndi mtsogoleri wa mpingo wa ECG – The Jesus Nation, lero wagawa chimanga kwa anthu opitilira 1300 mdera la Sub-T/A Nkhanga m’boma la Nkhotakota.
Polankhula pa mwambo ogawa chimangacho kudzera kwa mneneri wawo, a Aubrey Kusakala, prophet Bushiri wati ndiokhudzidwa kwambiri ndi kutaika kwa miyoyo komaso kuonongeka kwa katundu kamba ka madzi osefukira omwe akhudza bomali.
A Kusakala ati a Bushiri apeleka thandizo la chimanga kwa anthuwo ngati njira imodzi yowalimbikitsa kuti akhale ndi chiyembekezo komanso chikhulupiliro kuti Mulungu asintha nyengo zawo ndipo abwezeretsa zonse.
“Mawu amene a Prophet andituma kwa anthu amdela lakuno ndi okuti, ali nawo mmapemphero ndipo Mulungu abwenzeretsa zomwe ataya kamba ka kusefukira kwamadzi komwe kwapangitsa anthu ambiri kutaya katundu wawo”, atero a Kusakala.
A Bushiri kudzera kwa a Kusakala, alimbikitsabe anthu mdziko muno kuti asaleme ndikuthandiza anthu omwe akuvutika ndi vuto la njala lomwe lakuta dziko lino.
Mmawu awo a Group Village Headman Kakopa, athokoza prophet Bushiri ponena kuti thandizoli lafika munthawi yake pomwe anthu mdera nawo akhudzidwa kwambiri ndi njala ya dzaoneni.
Iwo anagwirizana ndi a Bushiri popempha anthu kuti asatope kuthandiza onse omwe akhudzidwa ndi njala ponena kuti ntchito ya mtunduwu siyosiyira munthu m’modzi yekha.
Malingana ndi a Kusakala, sabata ino yokha, galimoto zikulu zikulu zokwana khumi ndi ziwiri ndi zomwe zapita mmadera osiyana-siyana kukagawa chimanga kwa anthu ovutika.
Pakadali pano ndondomeko yogawa chimangayi yomwe Bushiri anakhazikitsa mwezi watha,yafikira ma boma ngati Zomba, Nkhota-kota, Nkhatabay, Rumphi Lilongwe, Nsanje , Thyolo, Mulanje, Ntcheu, Karonga komanso Mangochi, ndipo ntchitoyi ikupitirilabe.