Nthungululu komanso malikhweru ku Balaka: Escom yakonza vuto la magetsi

Advertisement

Kudamveka kufuula mwa chisangalalo pamene azimai adaimba nthungululu komanso malikhweru adamveka pakati pa abambo ndi achinyamata pamene kampani ya Escom imakonza vuto la magetsi lomwe lidali ku Majiga 2 ntauni ya Balaka.

Anthu okhala mdelari akhala opanda magetsi kwa mwezi wathunthu malingana ndi kuonongeka kwa makina a Transformer omwe adapsa. Izi akuti zidakhudza kwambiri anthuwa m’moyo wawo watsiku ndi tsiku chifukwa ntchito zawo zosiyanasiyana zidasokonekera.

Malawi24 itakayendera pa malo pomwe makinawa adawonongeka kummawaku, idapeza anthu ogwira ntchito ku kampani ya Escom akumangilira makinawa, zinthu zomwe zidapangitsa anthu ozungulira kuvina mochititsa kaso kwinaku akuimba nyimbo zotamanda akamunawa.

Izi zikudza pamene dzulo anthu okhudzidwawa adakachita m’bindikiro ku ofesi ya Escom pa tawuni ya Balaka ndipo adatseka zipata zonse zolowera ku ma ofesiwa zomwe zidapangitsa ogwira ntchito ku kampaniyi kuti alephele kulowa ku ma ofesiwa.

Komabe, zidatengera akuluakulu a pamalopa komanso nthumwi za anthu odandaulawa kutsekelana mkachipinda komata komwe adakambirana za tsogolo la nkhaniyi. Pamapeto pake, mbali ziwilizi zidasainilana mgwirizano omwe kampani ya Escom idalonjeza kuti ikhala itakonza vutoli pofika lolemba sabata ya mawa.

A Rhosario Chinkonda ndi ochita malonda mdelari. Iwo akuti vuto la magetsi lapangitsa kuti ataye ndalama za nkhaninkhani kudzera mu katundu yemwe waonongeka.

“Vuto la magetsi landibwenzera m’mbuyo ine ngati ochita malonda. Ndinali ndi katundu wambiri yemwe amafunika kukhala pa malo ozizira nthawi zonse. Komabe, katunduyi waonongeka zomwe zapangitsa kuti nditaye ndalama zankhaninkhani, adafotokoza a Chinkonda.

Ndipo m’mawu ake, mtsogoleri wa nzika zokhudzidwa ndi vuto la magetsili a Pretorius Halidi adayamikira m’gwirizano omwe anthu okhudzidwawa adali nawo. Iwo adati zikanakhala zovuta anthuwa kupeza chipambano chotelechi popanda m’gwirizano wabwino. A Halidi adayamikiranso kampani ya Escom pomva madandaulo awo komanso kuthana ndi vutoli.

Malawi24 yatsimikiza kuti vutoli lakonzedwadi ndipo magetsi akuyaka.

Advertisement