Flames yamaliza kuigwira ntchito Comoros

Advertisement
Flames

Timu yayikulu ya mpira wa miyendo ya Malawi ‘The Flames’ lero yakwapulanso Comoros ndi zigoli ziwiri kwa chete chete (2-0), mu mpikisano wa CAF African Nations Championship-CHAN pa bwalo la Bingu mu nzinda wa Lilongwe.

Zigoli za osewera wa Bullets Wongani Lungu pa mphindi ya chi 50′ ndipo patangodutsa mphindi 9 anabwera Binwell Katinji kudzasiya kukamwa yasa timu ya Comoros ndipo zigoli 2-0 pakutha pa mphindi 90 ndi zisanu zowonjezera zonse m’bwalo.

Mphunzitsi wa Malawi Kalisto Pasuwa anayambitsa George Chikooka pa golo, MacDonald Lameck, Maxwell Paipi, Lloyd Aaron, Nickson Mwase, Yankho Singo, Gaddie Chirwa, Binwell Katinji, Alick Lungu, Wisdom Mpinganjira ndi Wongani Lungu.

Timu ya Malawi sinawonetse chidwi mu mphindi za mchigawo choyamba mpaka masewelo anathera 0-0, ndipo mchigawo chachiwiri Malawi inadya moto kuti ipambane pomwe inakhazikika.

George Chikooka ndi goloboyi yemwe anawonetsetsa kuti anyamata a Comoros asapate chigoli ndinso kuti Malawi izigulire malo ku ndime ina oti ikalimbane ndi opambana pakati pa South Africa ndi Egypt omwe awumbudzane mawa lino.

Kupambana kwa Malawi kachiwiri pa Comoros zikutanthauza kuti yadzipezera zigoli zinayi kwa du (4-0) kutsatila chipambano cha (2-0) chomwe anapeza mkati mwa sabatayi pomwe amamenya ngati ali koyenda pa bwalo lomweli la Bingu.

Pa mphindi ya chi 74 Gaddie Chirwa anapeleka mpata kwa Chikumbutso Salima kuti ayeseko, pomwe Zebron Kalima ndi Ephraim Kondowe analowa m’malo mwa ogoletsa chigoli Binwell Katinji ndi Lloyd Aaron pa 78, ndipo kutulutsa komaliza kunali kwa Wongani Lungu yemwe anapeleka mpata kwa Chawanangwa Gumbo.

Chiyitengele timu ya Malawi Kalisto Pasuwa limodzi ndi omuthandizira ake Peter Mponda ndi Richard Mwansa sanagonjepo mu masewelo anayi onse omwe alamulira.