Khonsolo ya boma la Thyolo yapanga lamulo loti eni minda ikuluikulu ya tiyi adzipereka msonkho ku khonsoloyi.
Wapampando wa khonsoloyi, Rhustin Banda, ndiye watsimikiza za nkhaniyi. A Banda ati kwa nthawi yaitali eni mindayi samalipira msonkho wa pa chaka ku khonsoloyi ngakhale amapanga phindu lochuluka chifukwa chosowa lamulo.
“Minsonkhoyi ithandizira kupititsa pa tsogolo zitukuko za boma lino la Thyolo chifukwa thandizo lochoka ku boma la Constituency Development Fund (CDF) komaso District Development Fund (DDF) silikhala zokwanira kusintha miyoyo ya anthu,” anatero a Banda.
Mu mau ake, bwanankubwa wa boma la Thyolo, Hudson Kuphanga, wati khonsoloyi ikumana sabata ya mawa kumene adzakambirane pa kakhazikitsidwe ka lamuloli.
Minda ya tiyi yomwe ili ku Thyolo ndi monga Naming’omba, Satemwa, Eastern Produce ndi Conforzi.