Obera anthu ponama kuti mankhwala awo amachiza AIDS agamulidwa chindapusa cha K4.9 miliyoni

Advertisement

Bwalo la milandu la Senior Resident Magistrate m’boma la Mangochi, lagamula anthu awiri omwe amabera anthu ndalama pomanama kuti mankhwala omwe amagulitsa amachiza matenda a AIDS kuti alipile chindapusa cha ndalama zokwana K2,450,000 aliyese.

Posachedwapa, apolisi m’boma la Mangochi anamanga mayi Mary Saidi a zaka 25 komaso a Molly Kainga powaganizira kuti akhala akubera anthu ndalama pomawagulitsa mankhwala omwe amanama kuti amachiza matenda a HIV/AIDS.

Khothili linava kuchokera kwa oyimilira boma pa mlanduwu ochokera pa polisi ya Mangochi a Inspector Shadreck Wikisi kuti anthu ochanuka m’masowa akhala akumagula mankhwala otchedwa gentamicin ku ma “pharmacy” ndipo akatelo amaika chizindikiro cha “Gammora AIDS Cure” ndikumagulitsa pa mtengo wa K120,000.

Sabata yatha bwalori linapeza anthu awiriwa olakwa pa milandu yokwana isanu ndi umodzi (6) yomwe ndi kuphatikiza mlandu osintha zinthu zina pa mankhwala ndi wina opezeka ndi mankhwala popanda chilorezo ndipo Lachitatu pa 13 March, 2024, awiriwa anakaonekeraso kubwalori kuti akapatsidwe chigamulo chawo pa milandu iwiriyi.

M’chigamulo chake Senior Resident Magistrate Muhammad Chande, anati zomwe anachita anthu awiriwa ndi nkhanza ndipo zinali ndikuthekera kopangitsa kuti odwala matenda a kachilombo ka HIV asiye kumwa mankhwala oyenelera powona ngati athandizidwa ndi mankhwala abodza omwe awiriwa akhala akugulitsa anthu asanagwidwe.

Iwo analamula awiriwa kuti alipire K700,000 aliyense kapena akakhale kundende miyezi 24 pa mlandu woyamba wosokoneza zolemba za mankhwala, ndipo pamlandu wachiwiri wosunga mankhwala pamalo opanda ziphaso, awiriwa alamulidwa kuti alipire K350,000 aliyense kapena akakhale kundende miyezi 12 aliyese.

Pa mlandu wachitatu wogulitsa mankhwala popanda chilolezo chovomerezeka cha mankhwala motsutsana ndi ndime 56 ya lamulo la PMRA Act, awiriwa alipitsidwa K350,000 aliyense kapena kuti akakhale kundende miyezi isanu ndi umodzi, ndipo pa mlandu wa wachinayi otsatsa mankhwala popanda chilolezo motsutsana ndi Gawo 68 la PMRA Act, alipitsidwa K350,000 aliyense kapena akakhale kundende miyezi 12.

Awiriwaso alamulidwaso kulipira K350,000 wina aliyense kapena akakhale kundende miyezi isanu ndi umodzi pa mlandu wachisanu opereka mankhwala popanda chilolezo, ndipo pomaliza, alamulidwa kupeleka K350,000 wina aliyense kapena akakhale kundende miyezi 12 pa mlandu ofalitsa nkhani zabodza zokhudzana ndi HIV/AIDS.

A Mary Saidi ndiochokera m’mudzi mwa Kalonga mfumu yaikulu Mponda m’boma la Mangochi, pomwe a Molly Kainga ndiochokera m’mudzi mwa a Kalilombe mfumu yaikulu Chakhumbila m’boma la Ntcheu.

Advertisement