A Malawi omwe amafuna kuboola mtambo koma anakhudzidwa ndi kusokonekera kwa sisitimu ya nthambi yoona za anthu olowa ndi kutuluka ya DICS, atha kuusa moyo tsopano poti nthambiyi yati yayambiraso kusindikiza komaso yatsitsa mtengo wa ziphaso zoyendera.
Sisitimu ya DICS inasokonekera m’mwezi wa January chaka chino ndipo zakhala zikuveka kuti akathyali ena ndi omwe anapanga izi ndipo amalamura boma la Malawi kuti lipereke ndalama yokwana K2 biliyoni kuti sisitimuyi ibwezeretsedweso.
Kuchokera pa nthawiyo, nthambiyi yakhala ikugwila ntchito yobwezeretsa sisitimuyi ndipo posachedwapa akatswiri ochokera ku maunduna komaso nthambi za boma zingapo analowelerapo pa ntchitoyi kufikira lero pomwe nthambiyi yalengeza kuti chili chonse chili nchimake tsopano.
Kudzera mu kalata yomwe wasainira ndi mkulu wa nthambiyi a Charles Kalumo, nthambiyi iyambiraso kusindikiza ziphaso zoyendera sabata ino koma ati kwa pano ziphasozi zizisindikizidwa kaye ku ma ofesi ake aku Lilongwe okha kufikira mtsogolomu zonse zikatheka bwino bwino.
Kupatula apo, nthambi ya DICS yalengezaso kuti kuyambira pano, boma la Malawi latsitsa mtengo wa ndalama yomwe anthu amalipira akamapangitsi ziphaso zoyendera kwa a Malawi onse kuchoka pa K90,000 kufika pa K50,000.
“Nthambi yoona za anthu olowa ndi kutuluka, ikufuna kudziwitsa anthu onse kuti ntchito yokonzanso sisitimu yosindikizira ziphaso zoyendera, yatha. Izi zikutanthauza kuti ntchito yosindikiza mapasipoti ku nthambiyi yayambiranso ndipo kusindikiza mapasipoti ayamba pang’onopang’ono mumzinda wa Lilongwe m’sabatayi mpaka m’zigawo zina.
“Kupitilira apo, nthambi ndiyokondwa kudziwitsa anthu kuti boma lachepetsa mtengo wolipira popanga pasipoti ndi 55% kwa a Malawi onse, kuchoka pa K90,000 kufika pa K50,000, pa ma pasipoti wamba okhala ndi nthawi yodikirira ya masiku 10 pamene sisitimuyi ikabwelera bwino,” yatelo mbali ina ya kalatayi.
Nthambiyi yati zambiri zidzalengezedwa posachedwa pomwe nduna ya zachitetezo cha dziko komaso unduna ya ma uthenga adzachita msonkhano wa atolankhani, koma nthambiyi yapitilira ndikuthokoza anthu onse okhudzidwa chifukwa cha kudekha kwawo pa nthawi yomwe sisitimuyi inasokonekera.