M’busa wanjatidwa atagwidwa akuba mawaya amagetsi

Advertisement

M’busa wa mpingo wa Bua African Abraham ali m’chitokosi cha apolisi ku Mchinji kaamba koganizilidwa kuti adaba mawaya amagetsi wa ndalama zokwana K297,000 a bungwe lopereka magetsi la Escom.

Mneneri wa apolisi m’bomali watsimikiza zankhaniyi ndipo wati oganizilidwayu ndi a James Solomon a zaka 46 zakubadwa ndipo awagwira m’bandakucha wa lero pomwe iwo amasolola wayayu omwe ndi otalika pafupifupi mamita okwana 60.

Ndipo malipoti ena akuti m’mbuyomu m’busayu adagwirapo ntchito ku bungwe lopereka magetsiri.

M’busayu akuyembekezeka kukaonekela ku bwalo lamilandu ndikuyankha kukayankha mulandu wakuba zipangizo zamagetsi.

Iye amachokera m’mudzi mwa Chakuma kwa mfumu yaikulu Nkhumba ku Phalombe.

Advertisement