Sukulu za pulayimale zomwe ophunzira amuna akuvala ma buluku ngati yunifolomu azichenjeza

Advertisement

Sukulu za pulayimale za boma zomwe ophunzira ake amuna anayamba kale kuvala ma yunifolomu a ma buluku, zachenjezedwa ndi unduna wa maphunziro kuti zisiye ponena kuti pakadali pano lamuloli silinakhazikitsidwe.

Chaka chatha, phungu wa nyumba ya malamulo ochokera m’dera la Zomba Thondwe, a Roseby Gadama anapeleka maganizo m’nyumba ya malamulo kuti boma la Malawi liyambe kulora ophunzira achimuna m’sukulu za pulayimale, kuvala mathalauza ngati yunifolomu.

A Gadama anauza nyumba ya malamuloyi kuti maganizo oti ophunzirawa aziloledwa kuvala mathalauzawa anabwera poganizira kuzizira kwa madera ena m’dziko muno zomwe anati sizimagwira kuti ophunzira aku pulayimale omwe ambiri amakhala achichepele, adzivala yunifolomu ya makabudula.

Koma pomwe akuluakulu aku unduna wa maphunziro akukambirana ndi mbali zonse zokhudzidwa za tsogolo la maganizowa, Malawi24 yapeza kuti sukulu zina za pulayimale zomwe zili m’manja mwa boma, ophunzira amuna anayamba kale kuvala ma yunifolomu a mabuluku.

Tsamba lino litafusa ofalitsa nkhani ku unduna wa maphunziro, a Mphatso Nkuonera, atiuza kuti undunawu sukudziwa kuti izi zili chonchi koma sanafune kupsatira mawu ponena kuti sizikuyenera kukhala chonchi.

A Nkuonera anati nthawi zonse pakakhala nkhani yofuna kudziwitsa anthu mdziko muno, undunawu umatulutsa kalata yomwe akuti pa nkhani iyiyi siinatulutsidwe zomwe akuti zikutanthauza kuti sukulu zomwe ophunzira ake amuna akuvala ma buluku ngati yunifolomu, akuphwanya malamulo.

“Ineyo zoti pali sukulu zina zomwe ophunzira ake amuna akuvala mathalauza ngati yunifolomu, sindikudziwa nde kuti omwe akutelowo akupanga asanalamulidwe. Nkhaniyi tikukambilanabe ndi mbali zonse zokhudzidwa chifukwa tikufuna kuti aliyese ayikepo maganizo potengera kuti ndi nkhani yokhudza dziko lino.

“Unduna wa maphunziro umagwira ntchito motsogozedwa ndi malamulo ndipo pakakhala nkhani iliyose timatulutsa kalata (circular) ndipo pa nkhani imeneyi palibe kalata yomwe tinatulutsa yolamura kuti ophunzira amuna aku pulayimale atha kumavala mathalauza ngati yunifolomu. Amene akutelowo akupanga zimenezo mwakufuna kwawo. Tiyeni tidikile kalata kuchokera ku undunawu pa nkhani imeneyi,” watelo Nkuonera.

Ofalitsa nkhaniyu anati nkhaniyi itha kutenga nthawi yaitali kuti ithe kamba koti pali magulu ochuluka omwe akuyenera kuyikira mlomo  ndipo wati undunawu sukufuna kuti magulu ena adziuyimbe milandu kuti anasiyidwa kunja, osapereka maganizo pa nkhaniyi.

Advertisement