Ralph Mhone , Mganda Chiumia ndi Welani Chilenga alowa MCP

Advertisement

Mphekesera zikumveka kuti a Ralph Mhone , Mganda Chiumia ndi Welani Chilenga alowa chipani cha Malawi Congress (MCP).

Ena omwe mphekesera zikusonyeza kuti alowa MCP ndi katswiri odziwa kuyimba nyimbo zanthetemya zochemerera chipani a Miriam Chimbalanga.

Malingana ndi malipoti omwe matsamba ena atsindikiza, anthuwa alandilidwa ndi chipani pompano.

Chipani cha MCP chakhala chikulandila anthu ambiri odziwika bwino pa ndale monga Wachiwiri kwa Mkulu wa nyumba ya malamulo  a Mcheka Chilenje. Posachedwapa, MCP inalandilanso yemwe anali wachiwiri kwa Mtsogoleri wa chipani cha Democratic Progressive (DPP) a Uladi Mussa , Wapampando wa chipani cha UTM mu chigawo cha pakati a Samson Mithenga ndi wena.

Katswiri wa zandale wakhala akuuza olemba nkhani kuti Chipani cha  MCP chikupanga chikoka kamba ka utsogoleri wabwino wa Dr Lazarus McCarthy Chakwera.

Advertisement