Nzika zokhudzidwa zichita m’bindikilo ku maofesi onse a Immigration

Advertisement
Malawi Immigration offices in Lilngwe

Anthu ena omwe akudzitchula kuti nzika zokhudzidwa ati achita m’bindikilo kuma ofesi onse a nthambi yowona zolowa ndi zotuluka ya DICS pofuna kukakamiza mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera kuti achotse ntchito mkulu wa nthambiyi komaso nduna yokhudzidwa.

Izi ndi malingana ndi chikalata chomwe nzika za nchigawo chakum’mwera zalembera khonsolo ya mnzinda wa Blantyre komaso nthambi ya a polisi kupempha chilolezo chochititsa m’bindikilowu ku ma ofesi a nthambi ya DICS omwe ukuyembekezeka kuyimba sabata ya mawa pa 12 March.

Mwazina, nzika zokhudzidwazi  zikudandaula za kuyimitsidwa kwa ntchito yosindikiza ziphaso kamba ka kusokonezedwa kwa sisitimu ya nthambi ya DICS m’mwezi wa January chaka chino ndi a kathyali ena.

Mu kalatayi yomwe yasayinidwa ndi a Oliver Nakoma, Edwards Kambanje komaso a Sheik Aman Omar omwe ndi ena mwa akuluakulu onwe akutsogolera zionetselozi, nzikazi zati mkulu wa nthambi ya DICS a Brigadier Charles Kalumo komanso nduna ya za chitetezo cha mdziko a Ken Zikhale Ng’oma, alephera ntchito zawo.

Anthuwa ati makosana awiri amenewa akuyenera kuchotsedwa ntchito kuti apeleke mpaka kwa anthu ena omwe ali ndikuthekera kuti atha kugwira bwino ntchitoyi mokomera a Malawi onse mdziko muno.

“Mogwirizana ndi ndime 38 ya malamuro a dziko lino, tikukonzekera kukhala ndi m’bindikilo kunja kwa ofesi ya immigration ku Blantyre kuyambira pa 12 March, 2024 kuyambira 9:00am. M’bindikilo umenewu cholinga chake ndi kuuza mtsogoleri wa dziko lino kuti achotse wamkulu wa nthambi yowona zolowa ndi zotuluka komanso nduna yokhudzidwa chifukwa cholephera ntchito yawo.

“Tikuona kuti nthawi yakwana yoti apeleke mpata kwa anthu ena omwe akhozaso kugwira bwino ntchitoyi, potsatira zovuta zomwe zikupitilira pakupanga ndi kupezeka kwa mapasipoti. Tawona kuti anthu akuponderezedwa chifukwa cha anthu ena osachita bwino omwe amagwira ntchito ku dipatimenti yoona za anthu olowa ndi otuluka  m’dziko muno,” yatelo kalata ya nzika yokhudzidwazi.

Anthuwa ati adzachoka ku ma ofesi a DICS pokhapokha ngati zofuna zawo zitakwaniritsidwa ponena kuti a Malawi akuyenera adindo omwe amaika chidwi cha anthu pamtima komanso okhawo ofunitsitsa kutumikira osati kutumikiridwa.

Advertisement