Namandingo wati 2030 boma

Advertisement
Namadingo said this in Times Exclusive interview with Brian Banda aired on Times Television on Saturday.

“Mwayamba za ndale?” Anthu angoti kukamwa pululu pamene Dr Namadingo amene amadziwikanso bwino ndi dzina loti Doc walengeza  kuti “2030 boma” ndipo anthu akhale tcheru.

Izi zadzetsa mafunso ochuluka kwa anthu amene amamutsatira bwino.

Namadingo wanena izi kudzera pa tsamba lake la mchezo la Facebook lero chakumadzulo ano, pamene iye wangolemba kuti “2030 Boma.”

“Mwayamba za ndale?” A Kelvin Chimtendere m’modzi mwa anthu omwe amatsatira Namadingo afunsa funsoli kudzera mugawo la ndemanga.

Munthu wina anati Namadingo akungonena zocheza koma oyimbayu anayankhapo kunena kuti anthu atsekule maso ndipo akhale tcheru.

Namadingo ndi woyimba m’modzi yemwe ndi odziwika bwino m’dziko muno ndi nyimbo zake monga Maury, Nge, komanso Sakaka ndi zina zambili.

Mu chaka cha 2021, mneneri wina adanenelapo kuti Namadingo adzasankhidwa kukhala mtsogoleri wa dziko lino mu chaka cha 2025.

Advertisement