Bambo wafa ndipo anthu 6,145 akusowa mtengo wogwira kamba kakusefukira kwa madzi m’boma la Nkhotakota

Advertisement

Munthu m’modzi wafa pamene ena 6,145 manja ali ku nkhongo pamene akusowa pokhala kutsatira kusefukira kwa madzi komwe kwa chitika ku Dwangwa m’boma la Nkhotakota.

Malingana ndi lipoti lomwe lachokera ku khosolo ya bomali kudzera ku nthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzi, madera omwe akhudzidwa ndi ngoziyi ndi kwa mfumu yaikulu Kanyenda komanso Mphonde.

Munthu m’modzi amene wafayu ndi mulonda amene amagwira ntchito pa malo ogona alendo a Victorious Lodge ku Dwangwa ndipo wafa kutsatira bwato lomwe adakwera litatembunuzika.

Ndipo lipotili lati anthu okwana 4,985 ndi omwe akusowa pokhala ku Dwangwa kwa mfumu yayikulu Kanyenda.

Anthu okwana 957 ndi a m’mudzi mwa Mphonde pamene ena 67 ndi am’mdera la mfumuyi Malengachanzi.

Asilikali adziko lino apulumutsa anthu ena pafupifupi 200 omwe anazungulidwa ndi madzi.

Advertisement