…akuti “a Malondera analemba zigawenga”
Ya pa chiweniweni: phungu wa chipani cha MCP ku Dedza, a Willard Gwengwe omwe bokosi la maliro lomwe anagula lakanidwa mochititsa manyazi, aloza chala phungu nzawo wa chipanichi a Steven Baba Malondera kuti ndiye gwero la zonsezi ndipo akuti phungu nzawoyu sapambana chaka cha mawa chifukwa anthu asiya kuwakonda.
A Gwengwe omwe ndi phungu wa dera la Dedza Central, ayankhula izi kudzera mu kulipi (voice note) yomwe anthu akugawana m’masamba a nchezo momwe afotokoza tchutchutchu momwe zakhalira kuti bokosi la maliro lomwe anagula likanidwe ndikusiyidwa pansi Lachinayi pa 22 February, 2024 pa chipatala cha Kamuzu Central munzinda wa Lilongwe.
Munkufotokoza kwawo, a Gwengwe ati sabata yatha a mfumu a Kalonga anadwalika kwambiri ndipo anapempha a Baba Malondera omwe ndi phungu wa dera la mfumuyi lomwe ndi Lilongwe South-East, kuti awathandize ndi mayendedwe kuti apititse mfumuyi ku chipatala cha Kamuzu Central kuti akalandire thandizo la mankhwala.
Iwo ati chokhumudwitsa nchakuti phungu Baba Malondera anakana kupeleka galimoto yoti inyamule mfumuyi kupita ku chipatalako zomwe zinapangitsa akubanja kuyimbira foni a Gwengwe-wo kuti awathandize ndipo mosazengeleza nkuluyu anatumiza galimoto yake yomwe inakawasiya a mfumu a Kalonga ku chipatala cha Kamuzu Central komwe amwalilira Lachiwili lapitali.
“Ine atandiimbira foni powona ndi m’mene ndakhala ndikugwilira nawo ntchito, ndinatumizadi mayendedwe kukawasiya ku Kamuzu Central, koma a mfumu a Kalonga amwalira dzana (Lachiwiri). Dzulo (Lachitatu) ndalandira foni kuchokera kwa a Group a Nsendere, akubanja komaso a chipani kuti ndiwathandizeso kukanyamula maliro a mfumu a Kalonga komaso ndiwagulire bokosi nde ndinawauza kuti vuto palibe ndikuthandizani ngakhale kuti ndi dera la eni wake.
“Atava izi, olemekezeka a Malondera anandilembera ma message kundiopseza. Dzulo usiku cha m’ma 11, atuma zigawenga, kuzipatsa ndalama kukathyola nyumba ya a Group a Nsendere. M’mawa wa lero apeza zigawenga zina za ku Nchesi zina za ku Kamphata, kuzikweza mu lorry ndikuopseza mudzi onse ndi zikwanje kuti asalore galimoto yanga kugwira ntchito kumeneko pa maliro-po. Nde ine mafumu anandiuza kuti ndingozisiye ndipo ndinamuuzadi driver wanga kuti angokhale,” watelo Gwengwe.
Iwo anapitilira ndi kufotokoza kuti anali odabwa kuti a Malondera anathamangira kupititsa bokosi komaso galimoto kuti akanyamule zovutazo ku chipatalako ndipo akuti chinatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke nyanga nchakuti akubanja analamura kuti maliro akakafika ku mudzi, akachotse thupi la malemuwo mu bokosi lomwe anagula a Malondera ndikuliyika thupilo mu bokosi lomwe anagula a Gwengwe-wo.
Phunguyu wati, achinyamata omwe analembedwa ganyu ndi a Malondera atamva zomwe akubanja analamurazi, anakwiya ndipo anatenga bokosi lomwe anagula a Gwengwe ndikulitsitsa m’galimoto yomwe inanyamuka maliroyo, kwinaku akuwaopseza a Gwengwe-wo ndipo iwo ati zosezi ndi kamba koti anthu kudelari asiya kuwakonda a Malondera.
“Ine ndimafuna ndinene kuti, ngati anthu akukukana kuti sakukufuna, palibe chifukwa chomapangira zoyipa chifukwa pamapeto pake umakhala kuti ukudzionongera dzina. Ine ngakhale nditapanda kuyima koma a Malondera chaka cha mawa sawina chisankho. Ine ndinawamenya kale 2014, ndinawaluzitsa ma dera onse. Izizi akapitiliza ziwaonongera ambiri. Vuto lalikulu ndiloti a Malondera akudzipanikiza kuti anthu awakonde pamene anthu sakuwakonda,” anaonjezeraso a Gwengwe.
Malipoti akusonyeza kuti zonsezi zikuchitika kamba koti a Gwengwe akuwonetsa chidwi choti adzayimile ngati phungu wa nyumba ya malamulo ku delari pa chisankho cha chaka cha mawa, zomwe zikuoneka kuti sizikusangalatsa Baba Malondera.
Pakadali pano a Malondera sanalankhule za nkhaniyi.