Chiyipila Nsato ali m’manja mwa apolisi kamba kogwinya katundu ku wayilesi ya Radio Maria

Advertisement

Bambo wazaka 50 a Chiyipila Nsato, ali m’manja mwa apolisi ku Lilongwe kaamba kowaganizira kuti iwo ndi anthu ena atatu anakaba nawo katundu okwana 90 miliyoni kwacha ku likulu la tsopano la Radio Maria.

Mneneri wa apolisi mchigawo chapakati, a Foster Benjamin, atsimikiza zankhaniyi ndipo iwo atinso pakadali pano akwanitsa kupezapo zipangizo zina kuphatikizapo ma transmitter.

Pakadali pano a Nsato ali mmanja mwa a polisi.

A Nsato akuwaganizira kuti iwo akukhudzidwa pakubedwa kwa katunduyu ku maofesi atsopano a Radio Maria. A Nsato anachita umbandawu ndi anzawo ena atatu omwe pakadali pano apolisi ali mkati mowafufuza.

A Benjamin ati katundu onse omwe udabedwa ku ma ofesi wa ndi wandalama zokwana 90 miliyoni kwacha.

A Nsato amachokera m’mudzi wa Kamakoko kwa mfumu yaikulu Kwataine ku Ntcheu.

Advertisement