Tony Ngalande akhazikitsa mpikisano wa masewero msukulu za pulayimale

Advertisement
Member of Parliament for Balaka North Tony Ngalande

Phungu wa nyumba ya malamulo wa dera la kumpoto m’boma la Balaka olemekezeka a Tony Ngalande ati ndi Khumbo lawo kuthandizira kutukula masewero osiyanasiyana pakati pa achinyamata komanso ophunzira msukulu za pulayimale.

A Ngalande ayankhula izi lachisanu pamene amakhazikitsa chikho cha mpikisano wa mpira wa miyendo komanso manja chomwe ma timu ochokera msukulu zosiyanasiyana m’boma la Balaka alimbirane.

Chikhochi ndi Cha ndalama zokwana K3.5 million.

”Ndi kofunika kwambiri kuti ngati dziko tilimbikitse komanso kupititsa patsogolo maluso a masewero osiyanasiyana kwa ana achisodzera.Izi zili ndi kuthekera kotukula masewerowa mdziko muno,” adafotokoza a Ngalande.

Iwo adawonjezera kunena kuti kulimbikitsa ophunzira mu masewero osiyanasiyana kumathandiziranso anawa mu maphunziro awo.

Ndipo m’mawu ake, mkulu oyang’anira masewero osiyanasiyana msukulu m’boma la Balaka a Moses Arthur Chimbetete ayamikira phunguyi pokhazikitsa mpikisanowu ndipo ati izi zithandizira kwambiri pa chitukuko cha masewero komanso thanzi la ophunzira msukulu.

”Monga mukudziwa, timakhala ndi kuchepekedwa kwa zipangizo zothandizira m’masewero msukulu zathu. Chithandizochi chafika pa nthawi yake ndipo chithandizira kusula maluso osiyanasiyana.

A Chimbetete adamemeza adindo mu sukulu m’bomali kuti alimbikitse ophunzira kutenga nawo gawo mu masewero osiyanasiyana ponena kuti izi zingathandizenso kukweza chuma cha dziko lino.

Sukulu zokwana 28 zochokera mzigawo za maphunziro (zone) zokwana zisanu ndi zomwe zitenge nawo gawo mu mpikisanowu.

Pamapeto pa zonse, a Ngalande adapeleka mipira komanso ma yunifolomu a sukulu omwe agawidwe kwa ophunzira okwana 100. Iwo alonjezanso kupeleka ma yunifolomu ena 100 sabata la mawa

Advertisement