Anthu akudikila kuti adzasankhe ine, atero a shado a ku Zomba Thondwe

Advertisement

Yemwe akufuna kudzayimira chipani cha Democratic Progressive m’dera la Zomba Thondwe pachisankho chakunyumba yamalamulo mi chaka cha 2025 a Dumisani Lindani ati mosakayika konse iwo akudzapambana chisankhocho.

A Lindani awuza Malawi24 kuti pakali pano anthu a mdera la Zomba Thondwe akuchikonda chipani cha DPP pamodzi ndi mtsogoleri wachipanichi Professor Peter Muthalika ndipo anthu ambiri ndiwomwe adawapeza kuwapempha kuti adzakhale phungu wao wakunyumba yamalamulo kuyambira chaka cha 2025.

Iwo adatinso anthu a mdera la Zomba Thondwe akuvutika kwambiri monga kugona ndi njala komanso kukwera kwa zinthu zofunika pamoyo wamunthu m’dziko muno zapangitsa kuti anthu awakhulupilire kuti adzikawayankhulira zosowa zawo kunyumba yamalamulo.

A Lindani adadandaula kuti kusalandira kwama kuponi (coupon) ogulira zipangizo zotsika mtengo kwa anthu amdera la Zomba Thondwe kwapangitsa kuti mdelari kukhale njala yamgonagona chifukwa zikudziwikuratu kuti chaka cha mawa anthu adzavutikanso ndi njala.

“Anthu a mdera la Zomba Thondwe akungodikilira nthawi yachisankho chaka 2025 kuti adzasankhe ine mwana wao kuti ndidzakhale phungu wao komanso adzasankhe chipani chawo chokondeka cha DPP kuti chidzalowe m’boma.” Adatero a Dumisani Lindani.

Bungwe lowona zachisankho mdziko muno la Malawi Electroral Commission likuyembekedzeka kudzachititsa chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino, aphungu akunyumba yamalamulo komanso makhansala chaka cha 2025.

Advertisement