Anthu awili afa galimoto litagwera ku phompho


Anthu awili afa ndipo ena avulala pangozi yagalimoto yomwe yachitika lero pamudzi wa Machinga m’boma la Dowa mu nsewu wa Salima-Lilongwe pamene galimoto yomwe anakwera inalephera kukwera chitunda zomwe zinapangitsa kuti ibwelele m’mbuyo mpaka kukagwera ku phompho.

Mneneri wa apolisi ya Dowa Alice Sitima watsimikiza za ngoziyi ndipo wati anthu awiri afawa ndi a Mathews Nekhantani a zaka 26 zakubadwa komanso Moses omwe amakhala kwa mgona ku Lilongwe.

Malingana ndi mneneriyu, galimoto yomwe yachita ngoziyi ndi ya mtundu wa Hinno yomwe nambala yake ndi DA 1930 ndipo inanyamula anthu okwana 16 komanso matumba amakala ndipo imalowera ku Lilongwe pamene imachokera ku Salima.

Itafika pa mtunda wina pamudzi wa Machinga, inakanika kukwera ndipo inabwelela ndikugwera ku phompho.

Anthu awiliwa anavulala kwambiri m’mutu ndipo atathamangira nawo ku chipatala cha Dowa achipatala anatsimikiza kuti amwalira.

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.