A David Young atsanzika


Kazembe wa dziko la Amerika m’dziko muno, David Young, watsanzika potsatira kutha kwa nthawi yake ya ukazembe.

Mu chikalata chomwe ofesi ya ukazembe wa dziko la Ameleka yatulutsa chati a David akhala pa udindo wa ukazembe kwa zaka 34 ndipo tsopano apum.

Mu mawu awo, a Young ati ndi okondwa kuti atumikira anthu a dziko lino ndi la Ameleka ndipo pamene akupuma ali ndi chikhulupiriro kuti ubale wa maiko awiriwa ukhala ukupitilira.

Padakali pano Amy W. Diaz ndi amene ali pa udindowu malingana ndi uthenga omwe watsindikiziswa pa tsamba la pa Facebook.

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.