Boma lachititsa maphunziro a aphunzitsi a ophunzira amene ali ndi ulumali

Advertisement

Unduna wa za maphunziro mogwirizana ndi bungwe la Malawi Communication Regulatory Authority (MACRA) wakhazikitsa gawo lachiwiri la maphunziro kwa anthu amene amaphunzitsa chiyankhulo cha manja kwa anthu amene ali ndi ulumali .

Maphunzirowa amene akuchitikira Ku Mponela mu boma la Dowa athandizira kupitsa pa tsogolo kaphunzilidwe ka chiyankhulo cha manja kwa anthu amene ali ndi ulumali osamva.

Mu mau ake, wachiwiri kwa mkulu amene akuyang’anira maphunziro a Lucy Magagula anati unduna wa wa za maphunziro wadzipereka kuthandiza aphunzitsiwa kuti akhale ndi luso lokwanira lophunzitsa anthu aulumali mu chiyankhulo cha manja.

“Tachiyesa cha mwai kuti tibweretse maphunzirowa chifukwa athandizira kwambiri ana amene ali sukulu zosiyasiyana za anthu amene ali ndi ulumali,” anatero Magagula

Maphunziro akuchitika ndi nthandizo zochokera ku bungwe la MACRA komaso Universal Service Fund (USB).

Maphunzirowa akuyembekezeka kutha masiku asanu ndipo aphunzitsi okwana makumi asanu ndi awiri (70) ochokera ma boma khumi, asanu ndi anai (19) ndi amene akutenga nawo mbali.

Advertisement