Asakidwa ndi apolisi kamba ka kokupha mkazi wawo


Apolisi m’boma la thyolo akusaka bambo Nyozani Phiri a zaka makumi atatu zakubadwa powaganizira kuti ndi amene apha mkazi wawo wachinayi, Lucy San wa zaka makumi atatu zakubadwa.

Wachiwiri kwa mneneri wa apolisi m’boma la thyolo, sagenti Rebecca Kashoti, wati bambo Phiri anali ndi akazi anai ndipo mu usiku wathawu iwo anali pa mikangano ndi mkazi wawo wachinaiwu ndipo anamumenya mpaka kukomoka.

“Zitachitika izi a Phiri anathawa ndipo mwana wawo wa mwamuna ndi amene ananyamula mai ake kupita nawo ju chipatala ndipo achipatala anatsimikiza kuti mai wa amwalira” kuyankhula kwa Kashoti.

Bambo Phiri ndi ochokera mudzi mwa Musowa pamene malemuwa amachokera m’mudzi mwa Molande, mfumu yaikulu Nchilamwera boma la Thyolo.

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.