Chiyamba kale pa maimbidwe Lucius Banda watayira ka mtengo oyimba wamakono, Patience Namadingo, poyankhula zakupsa posachedwapa koma wadzudzula anthu mdziko muno kuti asiye mchitidwe oyika oyimba pa mpikisano.
Izi zili mu uthenga omwe Banda wayika pa tsamba lake la fesibuku Lachitatu pa 31 January, 2024 momwe amayamikira mfundo zokhwima komaso zogwira ntima zomwe Namadingo anayankhula mu pologalamu ya padera pa wayilesi ya Times.
Usiku wa Loweluka, pa 27 January, 2024, oyimba Namadingo amacheza ndi Brian Banda pa wayilesi ya Times ndipo mwa zina iye anafotokoza kuti kuchita bwino kwa oyimba anzake omwe atekesa pa Malawi pakadali pano, sikukuyenera kukhale chiopsezo koma chilimbikitso pa oyimba wina aliyese mdziko muno.
Poyankhula za nkhaniyi, Banda yemwe ndi wa mvula za kale pa nkhani ya maimbidwe mdziko muno, wati mfundo zochuluka zomwe Namadingo anayankhula mu pologalamu yapaderayi, zamugwira mtima kwabasi ndipo wamuvulira mwanayu chisoti.
Nzira zembe pamayimbidweyu yemweso amadziwika ndi dzina loti ‘Soldier’, wati yankho lomwe Namadingo anapeleka pa fuso loti kodi amaopsedwa ndi oyimba anzake omwe akuchita bwino pakadali pano omwe ndikuphatikizapo Driemo, wayankhira oyimba ochuluka.
“Ndakhala ndikusilira kaganizidwe ka mnyamatayu komaso kuthekera kwa kufotokoza mwaveveve pa zinthu zokhudzana ndi luso lathu la maimbidwe. Pakuyankhulana kwake ndi Brian Banda posachedwapa, ndiunikira funso limodzi lomwe adayankha lomwe ndikuganiza kuti adayankha kwa oyimba tonse.
“Atafunsidwa za kuchita bwino kwa Driemo kuposa kwake, iye anati (mwachidule) “kupambana kwa woimba m’modzi ndi chipambano cha oyimba onse,” haaa! Mwana iwe watiyankhila bwino zedi,” watelo Banda mu uthenga omwe anaulemba mchingerezi.
Mkuluyu yemwe pano watekesa pa Malawi ndi nyimbo ya chikondi ya ‘Umunyengerere’, sanalekere pomwepa koma kudzudzula a Malawi kuti asiye khalidwe lomawayika oyimba mdziko muno pa mpikisano zomwe wati ndizolakwoka kwambiri.
“A Malawi lekani kuwayika oyimba anu pa mpikisanu aliyense ndiwosiyana ndi nzake muzichitochito. Muwathandize ngati gulu la nkhondo kuti akwanitse kugonjetsa dziko la pansi. Zikomo Dr Namadingo. Ndikupitiliza kukudalitsa kuti upite ku malo osiyanasiyana kukagulitsa mbendera ya dziko la Malawi pa nkhani ya mayimbidwe,” wateloso Banda.
Namadingo wayankhula zokhudza mayimbidwe kwa nthawi yoyamba patadutsa dzaka zisanu, ndipo pakadali pano waneneratu kuti anthu asayembekezeso kuti posachedwapa amuwonaso akuyankhula pa wayilesi pa nkhani za mayimbidwe.