“Chakwera amange chipatala china nkuchitchula dzinalo” – atelo a Malawi ena

Advertisement
President of Malawi Lazarus Chakwera

Anthu ena mdziko muno awonetsa kusagwirizana ndi zomwe mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera achita posintha dzina la chipatala cha Phalombe kukhala John Chilembwe ndipo ambiri alangiza mtsogoleriyu kuti mwana omupeza sumamusintha dzina, umangolimbikira, n’kubala wako, n’kumupatsa dzina ukufunalo.

Izi zikudza pomwe a Chakwera Lolemba pa 15 January, 2024 alamula kuti chipatala chachikulu cha Phalombe chiyambe kutchulidwa kuti Chipatala cha John Chilembwe, kuyambira tsopano.

Iwo alankhula izi pa mwambo wa mapemphero okumbukira malemu m’busa Chilembwe omwe unachitikira ku Providence Industrial Mission (PIM) m’boma la Chiradzulu ndipo ati izi zichitike ngati mbali imodzi yokumbukira ndi kuyamikira ntchito yomwe malemu m’busa Chilembwe anagwira pothana ndi ulamuliro wa a tsamunda.

Koma nkhaniyi yabweretsa chinkulirano cha ndemanga zosiyanasiyana ndipo pomwe ena akuyamikira mtsogoleriyu kamba ka ganizolo, ambiri akuti uku ndikulakwitsa kwambiri pa umunthu.

Malingana ndi ndemanga zomwe tsamba lino likutsata m’masamba anchezo osiyanasiyana, a Malawi ambiri sakugwirizana ndi ganizoli kamba koti chipatala chomwe a Chakwera achisintha dzinacho chinamangidwa mu ulamuliro wa chipani cha Democratic Progressive (DPP) motsogozedwa ndi a Peter Mutharika.

Anthu ambiri ati kupeleka ulemu kwa malemu Chilembwe ndi ganizo la bwino koma ati kunali kwa bwino mtsogoleri wa dziko linoyu anakangomanga chipatala kufupi ndi PIM-ko ndikuchipatsa dzina lomwe akufunalo osati zomwe wapangazi ponena kuti uku kuli ngati kutola yophaipha.

Kudzera pa tsamba lake la fesibuku, katswiri pa nkhani za malamulo a Alexious Kamangila, wauza mtsogoleri wa dzikoyu kuti;  “Just build a modern hospital for him, if you truly want to Honour the man….bility. (Mungomumangira chipatala chake cha pa mwamba, ngatidi mukufuna kumulemekeza…. Kuthekera)”

Mbali inayi, tsamba linaso pa fesibuku lalemba kuti; “Akuti walamula kuti chipatala cha Phalombe boma chizitchedwa kuti John Chilembwe Hospital pamene Chilembweyo kwawo ndi ku Chirazdulu, bwanji osapanga chitukuko ku Chiladzuluko kuti azichitcha John Chilembwe? Zoona kukatenga chipatala cha boma lina kuti chizitchedwa John Chilembwe pali nzeru apa?” wadabwa munthu wina pa fesibuku.

Naye Bashir Al Bashir wanenetsa kuti; “Ife chathu ndi Phalombe District Hospital, mangani ku Chiradzulu chipatala chabwino muchitchule dzina la John Chilembwe. Kulemekeza John Chilembwe simulandu, koma tisamasinthe maina azinthu zoti zinamangidwa kale ndi ena just to score a point.

“Sinthani Chakwera Highway ikhale John Chilembwe Highway, it will carry weight, capital city, ukhala ulemu wamphanvu, osati mupangazi, khala ngati John Chilembwe ngwa Alhomwe, mwatisambula.

“Zinazi nzongopalana pakamwa, milomo yoyabwa kale, mumve tilankhula chani, mutinyapule, tisamavale tunduma dala, tikayankhula mutiloze, nokha kujambula video ya ma K1000 tikayankhula mukatineneze kudambwe, zopalana pakamwa ayi.

“Tikuthokoza Boma la DPP potimangira District Hospital, tinalibe, tinkadalira Ku Mulanje, musalowetse ndale, mukulakwa kwambiri, iyi ndi Phalombe District Hospital, ndipo ndife othokoza Ku Boma la DPP potipatsa chipatala.”

Komabe anthu angapo ati akugwirizana ndi izi ndipo munthu wina yemwe anaikira ndemanga za nkhaniyi, anati sakuonapo vuto lililose pa zomwe wachita Chakwera ponena kuti naye Mutharika mu nthawi yake anapanga zonga izi.

“Bingu Wa Mutharika adasintha dzina la Chipatala cha Bottom ku Lilongwe kuti chikhale Bwaila hospital. Adali ndi zifukwa zake… Mpaka Lero chimatchedwa Bwaila hospital. Lero asintha dzina la Chipatala kukhala John Chilembwe. Zusiyana pati? Tamatsatani history ya dziko lanu please,” watelo munthu wina.

Tsamba lino litaulutsa nkhaniyi, anthu anathamanga mwa nkokomo kuikira ndemanga ndipo mwa ndemanga 1000 zoyambilira zomwe anthu anayikira pa tsamba lino, anthu okwana 927 anasonyeza kusakondwa ndi ganizo loti dzinali lisinthidwe pomwe anthu okwana 49 anayikira kumbuyo ganizo la a Chakwera ndipo chiwerengero chotsalacho chomwe ndi 24, oyikira ndemangawo analemba zosagwirizana ndi nkhaniyi.

Advertisement