Apolisi ku mu Mzinda Lilongwe anjata anthu asanu ndi anayi (9) powaganizira kuti ndi mbava zomwe zimafuna kuba fetereza ndi chimanga ku kampani ya za ulimi ya Agricultural Research and Extension Trust (ARET).
Malingana ndi mneneli wa polisi ku Lilongwe a Hastings Chigalu ati anthuwa ananyamula zida zoopsa kuphatikizapo zikwanje ndi zitsulo zomwe amafuna kukatsekulira zitseko m’bandakucha wa loweluka
A Chigalu ati anthu akufuna kwabwino anatsina khutu apolisi kuti pali mbava zoopsa zomwe zimafuna kukaba kumalowo, ndipo apolisi anathamangirako ndikukabisala moyandikira.
“Cha m’ma 2 koloko m’mbandakucha, oganiziridwawa anafika pamalopo pa lorry yokula 15 tonnes yomwe ikuganizilidwa kuti amafuna kupakilira katundu” a Chigalu anafotokoza.
“Panthawi yomwe amafuna kuyamba kuthyola chipata cholowera kumalowo, apolisi anavumbuluka malo omwe anabisala, ndi kugwira oganiziridwa onse asanu ndi anayiwa ndipo Ali mchitolokosi mwathu” anatero a Chigalu
Anthu ochuluka mdziko muno akuyamikila ntchito zomwe apolisi akugwira mdziko muno pa nkhani ya chitetezo.
Masiku apitawa apolisiwa analepheretsanso mbava zina kuba ku kampani ya Museco Seed ndipo anamangapo anthu oganiziridwa atatu.