A Nankhumwa asankha Mneneli wawo

Advertisement
Ralph Jooma is a Mmember of Parliament in Malawi

Mtsogoleri wa mbali ya otsutsa boma  ku nyumba ya Malamulo muno mu Malawi a Kondwani Nankhumwa asankha phungu wa Nyumba ya Malamulo wa ku  dela la Mangochi Monkey-bay a Raph Jooma kukhala owayankhulira.

Malingana ndi chikalata chomwe chatuluka  lero pa 28 December 2023 ndipo  chasainidwa ndi ndi Mlembi wawo wamkulu a Dorothy  Kabango ati ntchito za a Jooma  zayamba m’mene kalatayi yangotuluka.

Kalatayi yati  ma uthenga onse okhudza ofesi  ya Mtsogoleri wa Otsutsa  boma zizipita Kaye kwa mneneli wawo a Ralph Jooma.

Advertisement