Mtsikana wadzikhweza atakalipilidwa kamba komwa mowa pa khilisimisi

Advertisement
Suicide

Mtsikana wa wazaka 16 m’boma la Mzimba wadzipha podzimangilira mu mtengo pafupi ndi nyumba yakwawo kamba koti mayi ake anamukalipira chifukwa chomwa mowa mwauchidakwa tsiku la khilisimisi.

Malingana ndi ofalitsa nkhani pa polisi ku Jenda m’bomali a Macfaren Mseteka, nkhaniyi yachitika pa dera lotchedwa Mqocha m’boma la Mzimba ndipo iwo azindikira malemuwa ngati Kellness Kajani yemwe anali ophunzira wa Form 1 pasukulu ya sekondale ya Robert Laws.

Ofalitsa nkhaniyu wauza nyumba zina zofalitsa nkhani mdziko muno kuti Lolemba lapitali lomweso linali tsiku lokwendwelera kubadwa Yesu Mkhristu, Kellnes anachoka pa nyumba ya makolo ake m’mawa kupita  ku malo ena kukamwa mowa ndi atsikana anzake angapo.

Apolisi ati Kellness anabwelera ku nyumba kwa makolo akeku usiku zomwe zinapangitsa makolo ake kukwiya kwambiri ndipo mayi ake anamukhalira pansi ndikumukalipira kuti asiye khalidwe lochititsa manyazili.

A Mseteka ati izi sizinasangalatse mtsikanayu ndipo Lachiwiri pa 26 December, 2023, anapakira zobvala zake zonse ponena kuti akupita kwa amalume ake ndipo chakumadzulo pa tsikuli, thupi lake linapezeka likulendewera mu mtengo wina pafupi ndi nyumba ya makolo akeyo.

Kellness Kajani amachokera m’mudzi mwa Kamangamadzi mfumu yayikulu Mbelwa m’boma la Mzimba.

Advertisement