Arava Farm yomwe ndi imodzi mwa kampani zomwe zatenga a Malawi kukagwira ntchito mdziko la Israel, yati anthu mdziko muno asadere nkhawa za umoyo wa azibale awowa ponena kuti anthuwa akugwira ntchito mosangala kwambiri, ndipo yatsutsa mphekesera zoti m’Malawi m’modzi waombeledwa ndi gulu la nkhondo la Hamas.
Wayankhula izi ndi m’modzi mwa akuluakulu a kampani ya Arava Farmers a Justice Kangulu omwe amayankhula potsatira mphekesera zoti m’modzi mwa achinyamata ochokera m’boma la Mangochi yemwe anatengedwa kukagwira ntchito za kumunda mdziko la Israel, waombeledwa ndi gulu la nkhondo la Hamas.
Nkhaniyi ikutsatira kanema (video clip) wina yemwe anthu akugawana m’masamba a nchezo, yemwe akuonetsa wachinyamata wa khungu la kuda akuzuzidwa ndi asilikali ena a gulu la Hamas ndipo pamapeto pake, anamuombera wa chinyamatayo.
Koma malingana ndi a Kangulu, palibe wachinyamata aliyese yemwe kampani yawo inamutenga kuchokera kuno ku Malawi kupita mdziko la Israel yemwe waombeledwa ndi gulu la Hamas ngati momwe ena akunenera, ndipo iwo anenetsa kuti mphekeserazi ndi bodza la nkunkhuniza.
Mkuluyu wati achinyamata omwe kampani yawo ya Arava Farmers inawapezetsa ntchito mdziko la Israel, akukhala mosangalala kwambiri ndipo watsimikizira anthu onse mdziko muno kuti asadere nkhawa za achibale awo omwe akugwira ntchito za ulimi mdzikolo.
“Palibe chifukwa chokhalira pa mpanipani kamba ka nkhani zonama. Onse omwe anakwera ndege yathu akugwira ntchito mosangalala m’minda yosiyanasiyana,” watelo Kangulu.
Kangulu anapitilira ndikufotokoza kuti a Malawi-wa atafika mdziko la Israel, analandilidwa ndi nduna ya dzikolo yowona za ubale ndi mayiko ena zomwe akuti ndi chisonyezo choti anthuwo akhala komaso kugwira ntchito motetezedwa.
“Onse ali m’malo otetezeka, alimi athu akudzipereka kuti awonetsetse kuti a Malawi onse ndi wina aliyense kuphatikizapo iwowo ali otetezeka. Kuti mumve zambiri zokhudza achinyamatawa omwe akugwira ntchito ku minda yathu, musachedwe kuyankhula nafe. Tidzakulumikizitsani ndikomwe anthuwa ali,” anaonjezera Kangulu.
Pomwe ntchito yotumiza achinyamata kukagwira ntchito ku Israel ikuyembekezeka kupitilira posachedwapa, boma la Israel komaso Malawi posachedwapa linatsindikanso za chitetezo cha a Malawi onsewa omwe akutumizidwa ku kukagwira ntchito Israel.