A Nankhumwa sangakatiwinitse ku chisankho za 2025, atero a Namalomba

Advertisement
DPP spokesperson Shadric Namalomba (C) and convention chairperson George Chaponda

M’modzi wa akuluakulu a chipani cha DPP a Shadric Namalomba ati mtsogoleri wa zipani zotsutsa boma Kondwani Nankhumwa sangakawanitse chipanichi ku chisankho cha 2025 ndi chifukwa chake iwo akufuna mtsogoleri wakale wa dziko lino a Peter Mutharika kuti akayimire DPP ndi cholinga choti chipanichi chilowenso m’boma.

A Nankhumwa anawonetsa chidwi chozapikisana ndi a Mutharika pa chisankho cha mtsogoleri wa DPP chaka cha mawa ndi cholinga chakuti azayimile chipanichi pa chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino za mu 2025.

Koma poyankhula pa msonkhano wa atolankhani lero, a Namalomba anati a Nankhumwa sangawadalire kuti alowetse DPP mu boma.

“Nanga alipo kumudziko akuti a Nankhumwa akhale mtsogoleri wa DPP? Chifukwa aliyense kumudziko akungoti pulofesa Arthur Peter Mutharika.

“A Nankhumwa afuna akatiluzitse? Ife tikufuna tikalowenso m’boma ndiye tikasankhe a Mutharika omwe a Malawi akuti ndi omwe angatilowetse m’boma,” anatero a Namalomba.

Iwo anadzdzuluanso a Nankhumwa kamba komangopita ku khothi kukasumila chipani zomwe anati zikubwezeretsa ntchito ya chipani.  

Dzulo, a Nankhumwa anapanganso  msonkhano ku Thyolo komwe ananena kuti DPP motsogozedwa ndi a Mutharika ikufuna ipangitse zisankho m’madera kuti asankhe atsogoleri atsopano mzigawo, m’maboma komanso  mu madera.

Malingana ndi a Nankhumwa, cholinga chake ndi chakuti asinthe maina a nthumwi zokavota ku msonkhano waukulu wachipanichi. Iwo anachenjeza kuti apita ku khoti DPP ikapanga zisankhozi.

Koma poyankhulapo, a George Chaponda omwe ndi wapampando wa konvenshoni ya DPP anati cholinga cha zisankhozi ndikuika adindo mu mipando yomwe adindo ena anachoka m’madera onse a dziko lino.

“Tikamapita ku konveshoni tikuyenera kuona kuti anthu okavota ku konveshoni alipo chifukwa ena anamwalira pamene ena anasiya chipani.

“Tiyeni tisamvere zomwe akunena a Nankhumwa chifukwa iwo akungofuna kusokoneza chipani,” atero a Chaponda.

Pothilirapo ndemanga, a Namalomba anati chipanichi chikuopanso kuti a Nankhumwa adzapita ku khothi kukasuma zokhudza konvenshoni ndi chifukwa chake chikufuna zonse ziyende mwa ndondomeko.

Advertisement