Pamene madera ambiri dziko lino akhudzidwa ndi vuto losowa mvula yokwanira, pali chiopsezo choti dziko lino likhala lopanda chakudya chokwanira chaka cha mawa.
Koma akatswiri pa nkhani za ulimi ati boma likuyenera kulimbikitsa alimi kuti azichita ulimi wa mthilira komanso alangiza alimi dziko lino kutsatira njira za makono za malimidwe ndi kugwiritsa ntchito mbeu zosachedwa kucha.
Mu sabata langothali, m’modzi mwa akatswiri pa nkhani za ulimi yemweso ndi mphunzitsi ku sukulu ya ukachenjedwe, Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources, Horace phiri wati nthawi yakwana tsopano kuti boma ndi alimi m’dziko lino agwirane manja potukula ulimi wam’thilira ngati dziko lino lili ndi masomphenya okhala ndi chakudya chokwanira mu chaka cha mawa.
“Inde mbeu zambiri zikuonongeka kamba ka dzuwa m’dziko muno, koma tikuyenera kupeza njira ina ya ulimi imene singadalire mvura imene imagwa mu nyengo yake.
“Alimi akuyenera kuzindikira kuti ulimi ndi bizinezi choncho akuyenera kutsatira njira za makono kuti azipeza phindu lochuluka komaso kupindulira dziko lino kukhala ndi chakudya chokwanira,” atero a phiri.
Boma kudzera mu nthambi ya za ulimi likulangiza alimi kuti atsatire njira za makono kamba koti dziko lino lakhudzidwa ndi dzuwa.
Mlembi mu unduwa wa za ulimi, Dickxie Kampani, walangiza alimi dziko lino kuti agwiritse ntchito mbeu zamakono zimene zimacha sanga.
A Kampani anati: “Kamba ka ng’amba yomwe ili m’dziko lino, tikulimbikitsa alimi kubzala mbeu zocha sanga, kugwiritsa ntchito manyowa amene amasunga madzi mu nthaka komaso malo amene amasunga madzi ndi amene akufunikira kuti abzalidwe mbeu.”
Alimi ambiri anayamba kubzala mbeu zawo kumapeto kwa mwezi wa November koma ma dera ambiri mbeu zawo zinapselera kamba ka dzuwa lochuluka ndipo akubzalaso ka chiwiri.
Wolemba: Peter Mavuto.