Kuyelekeza ndi mchaka cha 2017 pomwe oyimba otchuka Dan Lufani anatchuka ndi zithuzi zomwe anaima ndi nkazi wake wake nthawi imeneyo ali oyembekezera, ulendo uno oyimbayu sanapangeso zakezi ndipo gulu latutumuka pomwe langouzidwa kuti kwabadwa mwana.
Dan Lu pamodzi ndi nthiti yake Katerina Nzima lero alandira mphatso ya mwana wa mamuna zomwe anthu ochuluka adabwa nazo kwambiri potengera zomwe oyimbayu wakhala akuchita m’mbuyomu mkazi wake akayembekezera.
Mu January chaka cha 2017, Dan Lu anadzetsa mapokoso pa masamba a nchezo kamba ka zithuzi zosakhala bwino kwenikweni zomwe anaima ndi mkazi wake nthawi imeneyo, Emmie Kamkweche.
Nthawi imeneyo, Emmie anali oyembekezera ndipo awiriwa anatengana nkukajambulitsa koma anthu ambiri anatutumuka ndi zithuzizo kamba koti zina mwa zithuzizo zimaonetsa thupi la mayi oyembekezerayo yemwe pano si thupi limodziso ndi Dan Lu.
Pomwe ena amayembekezera kuti Dan Lu ndi bwezi lake lapano, Katerina apangaso zoterezi, lero awiriwa atutumutsa gulu ndi uthenga woti kwabadwa mwana wa mamuna.
Nkhaniyi yasangalatsa anthu ochuluka makamaka m’masamba a nchezo ndipo ena omwe ayikira ndemanga pa tsamba la fesibuku la oyimbayu pomwe analengeza za mphatsoyo, ati izi zikusonyeza koti oyimbayu akukhwima nzeru tsopano.
“Tiyamikire koti ulendo uno simunapangeso zija munapanga nthawi ijayi, Uku ndiye kukhala malume komaso kukhwima nzeru ndipo ife tasangalala nazo,” watelo munthu wina.
Anthu ena ati mwina zomwe zinachitika mu 2017 sizinachitike ulendo uno kamba koti Katerina ndi mayi amene amaoneka kuti ndi wakhalidwe labwino ndipo samafuna kusambula thupi lake.