Wapampando wa mabungwe omwe asali aboma ku Mzimba a Christopher Melele ati ndiwokhuzidwa kwambiri kuti adindo ena akulephera ntchito m’bomali.
Iwo adzudzula zomwe zikuchitika kuti apolisi ya Jenda akukanika kukwizinga mwana wa Inkhosi Khosolo wazaka 25 zakubadwa komanso yemwe ndiwogwira ntchito m’boma, pomwe maumboni woti munthuyo anakwatira msikana wachichepera wazaka 15,ulipo.
Melele wati sakuwona chifukwa chomwe apolisi akuchitira chidodo kukwizinga bamboyo.
“Ife ngati abungwe ndife wokhuzidwa kwambiri ndi zimwe zikuchitka kwa Jenda. Palibe munthu yemwe ali pa mwamba walamulo, tawona anthu a maina awo akumangwidwa ndiye apolisi akuwopa chani ku kumumanga wakunyumba ya chifumuyo?” anafunsa moteremo a Melele.
Melele wadzuzulaso ofesi yowona za chisamaliro cha wanthu komanso ana Social Welfare kuti akukanika kugwiritsa mphamvu za ofesiyo kuchitapo khanthu.
“Ndikudabwa kuti nkhani zina ofesi ya Social Welfare siyichedwa kuthamangirako koma apa kaya zikuwakanika bwanji, ife ngati amabungwe mbali yathu tachitapo kwatsalaku ndi a polisi ndi Social Welfare ofesi agwirepo ntchito” wanena moteromo Melele.
Miyezi iwiri yapiyi ofesi yowona za chisamaliro cha wanthu (Social Wilfire) idachita machiwi kukathetsa ukwati wa mwana wina ku Eswazini.
Mkulu wapolisi chigawo cha ku mpoto aKomishonala Kayira wati achitapo nkhanthu pa ndipo naye wasindika kuti palibe munthu yemwe ali pa mwamba pa lamulo.
Anthu ambiri m’bomali ali ndichidwi chofuna kuona kuti chilungo chikuchitika pa nkhaniyi.
Malawi24 ikutsatira mwachidwi nkhaniyi.
Wolemba Ephraim Mkali Banda.