Anthu a kwa Inkosi Khosolo ku Mzimba adzudzula apolisi a pa Jenda ponena kuti akulephera kumanga bambo wina yemwe anakwatira mwana wazaka 15.
Anthu akuganiza kuti apolisi akukanika kumanga bamboyo popeza ndi mwana wa a Inkosi Khosolo.
Nkhaniyi inavumbuluka ndi mabungwe womenyera maufulu a ana m’bomali.
Mabungwewo anachita chotheka kukamuchotsako mwanayo kubanjako koma chodabwitsa ndichakuti apolisi yakwa jenda akukanika kukwizinga bamboyo yemwenso ndiwogwira ntchito m’boma kunthambi ya nkhalango.
Apolisi ena womwe sanafune kuti maina awo adziwike awuza Malawi24 kuti akukanika kukamumanga mwana wa mfumuyo pachifukwa champhamvu ya mfumuyo.
Angakhale mwanayo anamuchotsako ku banjako, Mfumuyo akuti inaitanitsa kubwalo lake amai amwana ndi malume ake kuti asinthe zaka zakubadwa zamtsikanayo.
Inkosi Khosolo ndi mfumu imodzi yomwe yakhala patsogolo pothetsa maukwati woterewa koma panopa Mfumuyo ikuyikira kumbuyo mwana wake, zomwe anthu ena akuti sizikuyenera kutero.
Anthu ena kudelari apempha nduna yowona zakuti pasakhale kusiyana pakati pa mai ndi abambo komanso chisamaliro cha anthu kuti ilowerelepo pankhaniyi kuti chilungamo chiwoneke.
Anthuwo apitilizaso kupempha mkulu wa apolisi m’dziko muno mai Merlyne Yolam kuti alamule apolisi ya Jenda kukamanga mwana wa a Mfumuwa.
Wolemba: Ephraim Mkali Banda