Akatswiri pa chuma achenjeza anthu m’dziko muno kuti apewe kuononga ndalama mwachisawawa mu nyengo ya khirisimasi komanso mu chikondwerero cha chaka cha tsopano kamba kamavuto a chuma amene ali dziko muno.
M’modzi mwa akatswiriwa, a Lizzie Luhanga, ati anthu m’dziko muno ngati sasamalira ndalama zawo mu nyengo ya khirisimasi komanso mu chikondwerero cha chaka cha tsopano zidzetsa mavuto a zachuma m’maanja awo mu mwezi wa January.
“Pamene dziko lino lakutidwa ndi mavuto a zachuma, anthu akuyenera kusiya kuononga ndalama mwa chisawawa komaso kutenga nawo gawo mu zikondwerero zimene zilibe phindu pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku,” atero a Luhanga.
Iwo atiso anthu okhala m’mizinda ndi m’matauni m’dziko muno akuyenera kukhala ndi zichitochito zosiyasiyana zimene zingamabweretse ndalama pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku.
“Munthu akuyenera kukhala ndi zochita zosiyanasiyana ngati njira imodzi yothana ndi vuto la za chuma.
“Mwachitsanzo, anthu amene ali pa ntchito akhonza kuyamba bizinezi imene itha kuthandiza kuti azikhala ndi ndalama zokwanira pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku,” Iwo anatero.
Bambo Daniel Therenje ndi m’modzi mwa anthu ochita malonda mu msika mwa Manase mu mzinda wa Blantyre ndipo iwo ati mavuto a za chuma m’dziko muno afika poipa kwambiri ndipo izi ziyambitsa kuti ambiri achoke m’matauni kubwerera kumudzi
“Ife ochita bizinezi takhudzika kwambiri ndipo ngakhale kadyedwe pa khomo kasinthiratu. M’malo modya katatu pa tsiku, tikungogula mbatata kapena chinangwa ngati chakudya cha tsiku limenelo,” Iwo anatero.
Iwo atiso kuononga ndalama kamba ka chikondwerero cha khirisimasi kukhala kovuta kamba koti zinthu zambiri zakwera mitengo komanso tsiku tsiku mitengo ya zinthu ikumakwera maka m’ma shop a amwenye kumene amakaoda katundu wawo.
Mavuto omwe akhudza a Malawi ndi monga kukwera mitengo kwa katundu komanso kugwa mphamvu kwa ndalama ya Kwacha.
Posachedwapa, mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera anati a Malawi asataye mtima kamba koti dziko lino likulandira thandizo la ndalama kuchokera ku mabungwe ndi maiko akunja zimene zithandizire kubwezeretsa chuma cha dziko lino mchimake.