A Christopher Phiri azaka 40 zakubadwa yemwe ndi pulofeti wa mpingo wa Supernatural Embassy Ministrie, akusungidwa mchitokosi cha apolisi ku Mangochi kamba kogwililira mwana wawo obereka okha wazaka 16.
Malipoti akusonyeza kuti m’busayu wakhala akuchita pakati pa miyezi ya Sepitembala ndi Novembala chaka chomwe chino.
Malingana ndi kafukufuku wa apolisi, m’busayu banja lidatha ndi mkazi wake zaka ziwiri zapitazo ndipo wakhala akumukakamiza mwanayo kugonana naye.
Zadziwikanso kuti a Phiri amkamugona mwanayu pomuopseza kuti akapanda kutero ndiyekuti asiya kumulipilira sukulu fizi.
A Amina Tepani Daudi mwe ndi ofalitsa nkhani za a polisi m’boma la Mangochi ati apolisi apezanso zithuzi ndi makanema zomwe m’busayu amamujambula mwanayo.
M’busayu yemwe amachokera m’mudzi mwa Manjawira mfumu yayikulu Phambala m’boma la Ntcheu akaonekera ku kubwalo la milandu ndikuyankha mlandu ogona ndi mwana wake.