Khoti lidzapereka chigamulo mwezi wamawa kwa Sing’anga oganizilidwa kuti anagwililira atsikana awiri


Witchdoctor in red accused of raping tow children

Bwalo la High Court ku Zomba likuyembekezeka kudzapereka chigamulo chake pa 19 January 2024 kwa Sing’anga wina Malizani Chibingu Paoneka yemwe akumuganizila kuti adagwililira atsikana awiri apachibale osakwana zaka 18 zakubadwa.

Mu bwalo la milandu, oyimira Boma pamilandu adapempha bwalo kuti lipereke chilango chokhwima kwa Malizani Chibingu Paoneka chifukwa zomwe adachita ndidzosemphana ndi gawo 138 la buku loweruzira milandu yawupandu  ndipo adapempha oweruza kuti apereke chilango cha zaka 14 pamulandu uliwonse ndipo pamilandu yonse iwiri ayenera kukakhala kundende zaka 28 ndikukagwira ukaidi wakalavula gaga.

Koma loya yemwe akuyimira Sing’anga Paoneka yemwe ndiwochekera ku Legal Aid, Martin Dallas adapempha owerudza kuti asapereke chilango chokhwima popeza kupalamula uku kudali koyamba komanso kuti yemwe akumuyimilirayu adakali mnyamata choncho adapempha bwalo kuti lipereke chilango cha zaka 18 kwa Malizani Chibingu Paoneka pamilandu yonse iwiri.

Koma oweruza milandu yemwe akumva mulanduwu Justice Dick Sankhulani wati adzapereka chigamulo chake pa 19 January 2024 ndipo pakali pano Sing’anga Malizani Chibingu Paoneka akumusunga kundende ya Zomba.

Chipwirikiti chidabuka kunja kwa bwalo pomwe Malizani Chibingu Paoneka adafuna kumenya mtolankhani chifukwa chokuti amamutola zithunzi koma idzi zidalephereka chifukwa adali atamumanga unyolo.

Malizani Chibingu Paoneka adapalamula milanduyi mwezi wa April chaka chino m’mudzi mwa Diamon, mdera la Sub T/A Ntholowa Boma la Zomba.