Musawakwezere malipiro – yakuwa mokweza banki yaikulu

Advertisement
Secretary to the President and Cabinet, Colleen Zamba and UN representative in Malawi Rebecca Ada Donto

Banki yaikulu mdziko muno ya Reserve yalangiza boma la Malawi komanso ma kampani omwe siaboma kuti asakweze malipiro a ogwira ntchito awo nsanga ponena kuti zitha kusokoneza chuma cha dziko lino.

Izi zayankhulidwa lero mu mzinda wa Lilongwe komwe akuluakulu a banki yaikulu m’dziko muno ya Reserve anachititsa msonkhano wa atolankhani komwe anafotokoza zambiri zokhudza chuma cha dziko lino.

Malingana ndi mkulu wa bankiyi a Wilson Banda, ngati boma kapena makampani omwe siaboma angafulumile kukweza malipiro a ogwira ntchito awo, zipangitsa kuti boma likhale pa chintchito chobwereka ndalama zowalipilira anthuwo.

A Banda ati izi zitha kupangitsa kuti mavuto a zachuma m’dziko muno afike posauzana komaso wati zitha kupangitsa kuti anthu ochuluka achotsedwe ntchito kamba koti makampani ndi mabungwe adzisowa ndalama zowalipira anthuwa.

Iwo awuzaso atolankhani kuti ngati boma komanso mabungwe omwe siaboma angakweze malipilo a ogwira ntchito awo pano, katundu wambiri wa ma kampaniwa akhala okwera Kamba koti kuyendetsa bizinezi kukhala kovuta.

Advertisement