…yafotokoza cholinga choitanira Kell Kay, Lulu ku ‘show’ ya ‘gospel’
Gulu loyimba nyimbo za uzimu m’dziko muno la Great Angels Choir latsutsa mwantu wa galu mphekesera zoti gululi lagawanika komaso kuti lasintha dzina lake kukhala New Manna International Ministries.
Kuyambira sabata latha, m’masamba a nchezo mwakhala mukuyenda nkhani yoti gululi lasintha dzina ndipo onenawo amati mwambo osintha dzinali unachitikira pa Biwu CDSS yomwe ili kuseli kwa malo omwetsera mafuta galimoto a Total munzinda wa Lilongwe.
Koma poyankha za nkhaniyi, kwaya ya Great Angels yomwe ili pansi pa mpingo wa Church of Africa Presbyterian (CAP) kudzera mwa otsogolera mayimbidwe William Zonda, yati mphekesera zomwe zikuvekazi ndi bodza lankunkhuniza, anthu oyitsatira asazitengele.
Zonda yemwe amayankhula mu kanema yomwe anatulutsa kudzera pa tsamba la fesibuku la kwayayi, wati m’kwaya mwawo palibe munthu amene wachoka ndikukayambitsa gulu lina komaso wati palibe chikonzelo chili chose chosintha dzina lawo kukhala New Manna International Ministries monga momwe ena akufotokozera.
“Tikudziwa kuti muli ndi ufulu olemba, kaya analembayo ndi ndani, ife sitikumudziwa, sitingamuloze. Kumanena kuti Great Angels Choir ikusintha dzina a kuti kukhala chiyani kaya eni akewo. Ndikufuna ndikutsimikizileni a Malawi kuli kose komwe muli komaso ena amene mukutionera pano kuti zonse zimene mumaona sizoona.
“Pali ena angoganiza kuti tiyeni tipange ichi. Ndikunena kuti pano aliyese akumayenda ali ndi zifukwa zache muntima mwache, sitingamutsutse zolemba zake, koma kunena kuti nkhani yomwe analemba kuti Great Angels Choir yasintha dzina, aaa ayi. Nkhani imeneyo ndiyabodza. Ena akunenaso kuti anthu ena achoka mu Great Angels Choir akayambitsa zawo, ayi palibe wachoka tose tidakalipo ndipo tikukhulupilira kuti Great Angels Choir anayiyika ndi cholinga. Choncho nkhani yomwe munava kapena munawerenga kapena ena akuyankhula, imeneyo ndiyabodza,” anatelo Zonda mukanemayo.
Pofuna kutsindika kuti nkhani yoti kwayayi yasintha dzina ndiya bodza, Zonda anati Great Angels Choir siyamunthu m’modzi ndi gulu la anthu ambiri limene kutsogoloko kwake kuli akuluakulu amene amayang’anira ndipo ndiyolembetsedwa kotelo kuti ndikovuta kuti munthu m’modzi anganyamuke ndikusintha dzina la gululi.
Iye wati akuganiza kuti anthu amene akufalitsa nkhani yabodzayi ali ndimalingaliro ofuna kuyipitsa dzina la gululi ndicholinga choti ku phwando la maimbidwe lomwe kwayayi yakoza pa 25 December chaka chino munzinda wa Lilongwe, kusadzabwere anthu ochuluka kudzavina nyimbo zawo zotsitsimutsa.
Iye anayankhaso anthu omwe akudzudzula kwayayi pa zomwe yapanga zoitana anthu oyimba nyimbo za chikunja monga ngati Lulu, Kell Kay ndi ena kuti adzaimbe nawo kuphwando lamaimbidwe lawoli, ponena kuti ngakhaleso Yesu Mkhristu amene ankagwilitsa ntchito anthu owoneka ochimwa akufuna kukopa khwimbi la anthu kuti limutsate.
Zonda anati gulu lawo likufuna kudzatsitsimutsa anthu omwe amakonda komaso kutsatira oyimba ngati amenewa ndipo wati anthu asiye kuwaloza chala pa nkhani ngati iyi komaso wati anthu asadabwe posachedwapa akawona kwayayi atayitanaso oyimba wina oyimba nyimbo zachikunja.
“Enaso a kuti ndichifukwa chiyani mukutenga Kell Kay, aaa inu Kell Kay ndi mwana wa Mulungu, Kell+ Kay amapempheraso mwinaso enawa amawaposaso. Amene uja ndiofunikira kwambiri. Yesu Mkhristu ankagwiritsa ntchito anthu amaluso osiyanasiyana kuti anthu ena amumvere. Ife ngati Great Angels Choir timagwiritsa ntchito china chili chose choyenelera kuti moyo wa munthu upulumutsidwe. Mukaona kwabwera Kell Kay, Skeffa Chimoto, Lulu, Billy Kaunda musamadabwe.
“Iwowa ali ndi anthu amene amawatsata, nde ifeyo tikufuna anthu ngati emenewowo kuti tiwatumikire uthenga wa Mulungu. Ndipo mukhale pomwepo chifukwa tsiku lina muzaonaso pakubwera wina, anthu nkudabwa kuti zachitika bwanji awa kubwera ku show ya gospel. A khilisitu ambiri timakhala ndi tsankho koma ife sitili choncho, monga momwe amachitira Mulungu ifeso timasakasaka chotaikacho,” anateloso Zonda.
Apa anawonjezera kuti ichi ndi chifukwa chake kwaya yawo imapezeka malo aliwose amene ayitanidwa kuti akayimbe posayang’anira kuti wawaitana ndi ndani ponena amazindikira kuti ntchito yawo ndiyotembenuza anthu ochimwa mtima, kuti asiye zoipa ndikuyamba kumutsata Mulungu.