A Mutharika ati ndondomeko zomwe ayika a Chakwera ndizochepa

Advertisement
Peter Mutharika

Mtsogoleri wakale wa dziko lino a Peter Mutharika ati ndondomeko zomwe ayika a Lazarus Chakwera pofuna kuthana ndi mavuto omwe akuta dziko la Malawi ndizochepa kwambili.

Iwo ati mwandondomeko zina zomwe a Chakwera amayenera kuchita ndi monga kupereka ndalama ku masukulu awukanjende ndi cholinga choti pasakhale ophunzira osiya sukulu kamba ka fizi.

A Mutharika anatinso a Chakwera akuyenera kutsitsa mitengo ya mafuta komanso atsitse mtengo wa feteleza chimanga ndicholinga choti a Malawi ambili athe kukwanitsa kugula feteleza.

Iwo anatinso a Chakwera akuyenera kuchotsa abale awo omwe ntchito yawo nkudzangowononga ndalama. Malingana ndi a Mutharika, a Chakwera akuyeneranso kupereka ndalama ku bungwe la NEEF ndicholinga choti achinyamata ndi azimayi azitha kutenga ngongole kuti azichitira ma bizinezi

A Mutharika anapitilizanso kuti a Chakwera akuyenera kugwilira ntchito a Malawi osati banja lawo.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.