Zayambika: Mafuta a galimoto, magetsi akwezedwa mtengo

Advertisement
Malawian President, Lazarus Chakwera

Potsatira kugwa mphamvu kwa ndalama ya Kwacha, bungwe la Malawi Energy Regulatory Authority (MERA), lakweza mitengo ya magetsi ndi mafuta a galimoto ndi pafupipafupi 45 Kwacha pa 100 Kwacha iliyonse ndipo izi zikuchitika pomwe mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera ali kunja.

Malingana ndi kalata yomwe bungwe la MERA yatulutsa usiku wa lachinayi, kukwera kwa mitengo ya mafuta ku ndi kamba ka kugwa mphamvu kwa ndalama ya kwacha mwa zina.

Chikalata cha bungwe la MERA chomwe wasainila ndi Reckford Kampanje, wapampando wa board ya bungweli, kuyambira lero pa 10 November, 2023, petrol azigulidwa pa mtengo wa K2,530 kuchoka pa K1,746 ndipo wakwera ndi 44 Kwacha pa 100 Kwacha iliyonse.

Bungweli lati diesel wafika pa mtengo wa K2,734, kuchoka pa mtengo wa K1,920 komwe ndi kukwera ndi 42 Kwacha pa 100 iliyonse.

MERA yakwezanso magetsi kuchoka pa K104.46 pa kilowati iliyonse kufika pa K123.26 pa kilowati iliyonse. Kukwezaku kwachitika patadutsa miyezi iwiri chikwezereni mtengo wa magetsi.

Izi zachitika patangodutsa tsiku limodzi banki yayikulu ya Reserve (RBM) italengeza kuti ndalama ya kwacha yachepetsedwa mphamvu kuyelekeza ndi ndalama ya dollar ya ku America.

Banki ya RBM lachitatu pa 8 November, 2023 kudzera mu kalata yomwe inasainidwa ndi gavanala wake a Wilson Banda inati kuyambira lachinayi pa 9 November, 2023, ndalama ya dollar imodzi ya m’dziko la America (USD1) idzisinthidwa pa MK1700 kuchoka pa MK1180 zomwe zikuyimira kuchepa mphamvu ndi 44%.

Izi zikutanthauza kuti katundu wambiri m’dziko muno azikwera mtengo zomwe zikupeleka chiopsezo choti a Malawi omwe akuvutika kale akhale pachipsinjo chachikulu.

Advertisement