Mangani malamba: Kwacha yachepetsedwa mphamvu

Advertisement
President Lazarus Chakwera and Vice President Saulos Chilima have been ruling the country together since 202

Pamene zinthu zikuvuta kale, anthu m’dziko muno ayembekeze kuti zinthu zitha kufika pothina zedi kamba koti ndalama ya kwacha yachepetsedwa mphamvu kuyelekeza ndi ndalama ya dollar ya ku America.

Izi ndi malingana ndi chikalata chomwe banki yayikulu m’dziko muno ya Reserve (RBM) yatulutsa lachitatu pa 8 November, 2023 chomwe chasainidwa ndi gavanala wake a Wilson Banda.

Mukalatayi RBM yati kuyambira lachinayi pa 9 November, 2023, ndalama ya dollar imodzi ya m’dziko la America (USD1) idzisinthidwa pa MK1700 kuchoka pa MK1180 zomwe zikuyimira kuchepa mphamvu ndi 44%.

Akuluakulu a bank-yi ati chiganizochi chochepetsa mphamvu ndalamayi achipanga potsatira kafukufuku yemwe zotsatira zake anapeza kuti momwe ndalamayi akuyigulitsira, zusiyana kwambiri ndi momwe zinthu zilili pansika.

“Reserve Bank of Malawi (RBM) ikufuna kudziwitsa ma banki oyenelera kuti mitengo yosinthira ndalama yasinthidwa kuchoka pa MWK1180.29 kufika pa MWK1700.00 pa Dollar imodzi yaku United States kuyambira pa 9 November , 2023.

“Kusinthaku kwachokera ku kafukufuku wopangidwa ndi bankiyi yemwe adawonetsa kuti panali kusiyana kwa kapezekedwe ndi kufunidwa (supply-demand) kwa ndalamayi ngakhale panali kusintha kwamitengo yosinthira,” yatelo mbali ina ya Kalaya ya RBM.

Banki ya Reserve yati ipitilirabe kuwunika momwe msika osintha ndalama ukuyendera pofuna kupewa chipwirikiti pakati pa ochita malonda omwe angayambitse kusokonekera kwambiri.

Izi zikutanthauza kuti katundu wambiri atha kukwera mtengo m’dziko muno zomwe zikupeleka chiopsezo choti a Malawi omwe akuvutika kale akhale pachipsinjo chachikulu.

Advertisement