Msonkhano ku Saudi Arabia walepheleka, Chakwera apitabe?

Advertisement
Malawian President, Lazarus Chakwera

Pomwe mtsogoleri wa dziko lino analongedza kale zovala kuti anyamuke lero lachitatu kupita m’dziko la Saudi Arabia ndi anthu osachepera 70, msonkhano omwe amayenera kupitira wa Africa-Arab Summit walepheleka.

Lachiwiri sabata ino boma linalengeza kuti a Chakwera anyamuka Lachitatu kupita m’dziko la Saudi Arabia komwe akakhale nawo pa mkumano wa mayiko a mu Africa komaso maiko anchigawo cha ku m’mawa (middle east) omwe ukutchedwa ‘Africa-Arab Summit’.

Akuluakulu aboma, lachiwiri anauza atolankhani munzinda wa Lilongwe kuti msonkhanowu upereka mwayi kwa maiko a ku Africa kuphatikiza Malawi kuti alimbitse ubale wawo waukazembe ndi zachuma ndi dziko la Saudi Arabia lomwe lili likulu lazachuma ku Middle East.

Koma patangotsala maola ochepa kuti a Chakwera anyamuke kumapita m’dziko la Saudi Arabia, akuluakulu omwe amayendetsa zokozekera msonkhano wa Africa-Arab Summit, alengeza kuti mkumanowu wayamba wayimitsidwa kaye.

Malingana ndi nyumba zina zofalitsa nkhani zakunja, kuyimitsidwa kwa msonkhanowu omwe umayenera kuchitika pa 10 ndi 11 November, 2023, ndi kamba ka mpungwepungwe omwe uli kudera la Gaza m’dziko la Palestine pakati pa dziko la Israel ndi gulu la Hamas.

Ngakhale sanatchule tsiku lenileni, akuluakulu a dziko la Saudi Arabia ati nkumanowu omwe umayenera kuchitikira ku dera la Riyadh ukhalapo kutsogoloku koma ati ndikofunikra kuti nkumanowu usasokonezedwe ndi nkhondo yomwe yabukayo.

Boma la Malawi linalengeza kuti a Chakwera akuyenera kunyamuka pa bwalo la ndege la Kamuzu International mu nzinda wa Lilongwe lero nthawi ya 14:25 ndipo amayembekezeka kubwerera ku mudzi kuno Lachiwiri pa 14 November, 2023, nthawi ya 13:35.

Kupatula kupita m’dziko la Saudi Arabia, a Chakwera amayembekezekaso kukakhala nawo pa chiwonetsero chachitatu cha zamalonda Africa chotchedwa Intra-African Trade Fair (IATF2023) chomwe chichitikire ku Cairo m’dziko la Egypt kuyambira pa 13 November, 2023.

Pakadali pano boma silinabwere poyera ndi kufotokoza ngati mtsogoleri wa dzikoyu anyamukebe ulendo wake kapena ayi komwe akuluakulu a boma analengeza kuti akuyenera kunyamuka ndi anthu osachepera 70 omwe ndikuphatikiza nthumwi za makampani osiyanasiyana komaso akuluakulu a boma.

Ena mwa anthuwa monga mafumu ndi ogwira ntchito mu ma Khonsolo komanso ma dipatimenti a boma ali kale ku Saudi Arabia kudikira a Chakwera.

Advertisement