Magalimoto apachikidwa kaye: Mitengo ya mathalasipoti yakwera

Advertisement
Vehicles on a queue at a fuel service station in Malawi. The country has been facing recurring fuel shortages for close to two years

… Limbe-Chilimba pano ndi K2,500 kuchoka pa K1,000

Kupsa pamwamba ndi pansi pomwe ngati chigumu: anthu omwe apachika kaye magalimoto awo chifukwa chakusowa kwa mafuta alibe kothawira kamba koti wa minibasi ndi njinga za kabaza wakweza mitengo ya mathalasipotu mwa asafuna asiye.

Lero ndi tsiku lachinayi kusowa kwa mafuta a galimoto kutafika pa mponda chimera m’madera ambiri m’dziko muno ndipo munzinda wa Blantyre zinthu zafika pa mwana wakana phala.

M’malo mopezeka pamsewu, magalimoto ambiri mumzindawu akuwunjikana malo othilira mafuta, kudikilira kuti mwina nthawi ina a chita mwayi ndikumwetsa galimoto zawo za ludzuzo.

Mumzinda wa zachumawu, zafika poti anthu osaka mafutawo akumayenda ndi maguza komaso malilemba kupangira kuti zikavuta agone pa malo othilira mafuta aliwonse omwe akupeleka chiyembekezo.

Izi zapangitsa kuti anthu ena apange chisankho chongopachika kaye ma galimoto awo ndikuyamba kukwera ma minibasi komanso njinga za moto.

“Ineyo abwana galimoto ndili nayo komano zafikapa ndangoyisiya kaye, tiyambaso kuyendera mafutawa akayambaso kupezeka. Moti pano tikukwera kaye ma minibasiwa,” anatelo a Juma Sochera omwe tinawapeza mu tauni ya Blantyre akudikilira minibasi yopita kwa Kameza.

Iwo anati pomwe amaganiza kuti kukwera minibasi kuwathandiza kuseva ndalama komaso chipsinjo chosakasaka mafuta, mitengo ya mathalasipotiwo nayo yakwera mopeleka mantha kwambiri.

“Ndisaname zinthu zavuta, m’mbuyomu minibasi tikakwera mtauni muno kupita pa Kameza timalipira ndalama yosapitilira K600, koma pano akuti K2,000. Tili pa mavuto ndithu,” anawonjezera choncho a Sochera.

Nawo a Ruth Chitengu omwe akuti anakakamizika kukwera njinga ya moto kuchoka ku Limbe kufika mtauni ya Blantyre kamba kakusowa kwa ma minibasi, ati nawo anyamata a kabaza sakunyengelera potchaja mtengo.

“Ndipo ndadzimvera chisoni kuti pa Limbe pomwe timakwelera K500 lelo ndalipira K3,500, eee ndisaname ndine okwiya. Itangofika minibasi anthu kunali kukanganirana kukwera nde ine ndinangoti ndikwera njinga, koma eee! Ayi zikomo,” adandaura a Chitengu.

Pakadali pano chiwerengero cha anthu oyenda pansi makamaka maulendo afupiafupi mumzindawu chakwera kamba kakukwera mitengo kwa ma thalasipotiku.

Tsamba lino lapeza kuti kuchoka ku Limbe kupita mtauni ya Blantyre, anthu akulipira K1200 kuchoka pa K500, pamene kuchoka ku Chilimba kupita ku Limbe mtengo otchipitsitsa ukumakhala K2,500 kuchoka pa K1,000.

Nako ku Lilongwe vutoli silinawalambalare, ndipo kumenekoso mitengo ya maminibasi yakwera kwambiri.

Advertisement