Diamond Platnumz atutumutsa anthu pofika pa siteji ali m’bokosi

Advertisement
Diamond Platinumz gets out of coffin

..mwini wake wati nayeso zinamuwopsa

Gulu la anthu likupitilirabe kukambirana malodza omwe anapanga oyimba otchuka m’dziko la Tanzania Diamond Platnumz yemwe anafika pa malo oyimbira ali m’bokosi lomwe linanyamulidwa ndi anthu ovala zovala za makaka akuda.

Lamulungu lapitali pa 10 September, kunali phwando la mayimbidwe lotchedwa ‘Wasafi Festivals 2023’ ku Ruangwa m’dziko la Tanzania komwe anthu akuti awona malodza komaso malawulo.

Malingana ndi kanema yemwe tsamba lino lawona yemweso anthu ochuluka akugawana m’masamba anchezo, oyimba otchukayu anapita pa siteji (stage) kuti akayimbe atayikidwa m’bokosi la maliro lomwe linanyamulidwa ndi anthu angapo.

Sitejiyo inali ndi makaka akuda ndi njira yoyatsidwa ndi nyali ndipo mafupa angapo owoneka ngati a anthu (skeletons) anayikidwa panjira yokafikira pa sitejipo kwinaku nyimbo zina zochititsa mantha othetsa mankhalu zinali kuyimba, ndipo zinali ngati anthu akuwonera kanema.

Bokosilo linayimikidwa pa siteji molunjika pafupi ndi mabokosi ena ndi gulu la anthu omwe anavala zovala zakuda omweso amawoneka kuti anali ndi nkhawa komaso chisoni.

Pomwe anthu samadziwa kuti chikuchitika ndi chiyani, Diamond Platnumz adalumpha kuchokera m’bokosi lomwe anamuikamolo kwinaku atanyamula chinkuza mawu (microphone) ndipo anayamba kuyimba kwa anthu mazana mazana omwe anakhamukira pamalopo.

Poyankhula za nkhaniyi kudzera pa tsamba lake la Instagram, Diamond Platnumz adati kufika pa sitejipo ali m’bokosi sichinali chinthu chophweka ndipo wati anali wamantha nthawi yonse yomwe anali m’bokosimo.

“Kutuluka m’bokosi la maliro kunali kwamisala usiku wathawu (Sunday 10 September), ndinali wamantha kwambiri mmenemo! (Coming out from the Coffin was an insane Experience last night, was scared as f*ck in there!)” anatelo Diamond Platnumz.

Pakadali pano pali kusiyana maganizo za nkhaniyi kamba koti ena ati izi ndi ukadaulo ponena kuti zinaonjezera thendo la madyelero amayimbidwewo, pomwe ena akudzudzula mchitidwewu ponena kuti mabokosi amaliro asamagwiritsidwe ntchito ngati zosangalatsa chifukwa akuyimira kutayika kwa miyoyo.

Aka sikoyamba kuti m’dziko la Tanzania woyimba afike pa siteji ali m’bokosi kamba koti chaka chatha pa mwambo wa ‘The Afro East Carnival’, Ibrahim Abdallah Nampunga yemwe amadziwikanso kuti Ibraah, adalowa m’bwalo ali m’bokosi lamaliro.

Advertisement