Bambo wadzikhwezera mkachisi

Advertisement

Bambo wa zaka 45 m’boma la Thyolo wadzipha podzimangilira mkachisi kamba koti nkazi wake anapeleka ku kachisiko ndalama yose yomwe anapeza atagwira ganyu.

Nkhaniyi watsimikiza ndi mneneli wapolisi ya Masambanjati m’bomali, a George Kaleso, omwe azindikira mkuluyu ngati a Rex Kondwani omwe anali ochokera m’mudzi mwa Muwalo mfumu yaikulu Changata ku Thyolo komko.

A Kaleso ati masiku apitawa banjali lidagwira ganyu yolima m’munda wina mdera lomwelo ndipo anapatsidwa ndalama yokwana K12,000 ngati malipilo yomwe akuti amayisunga ndi mkazi wawo.

Apolisi ati a Kondwani posachedwapa anafusa akazawo kuti awapatse ndalama ina pa ndalama yomwe anapezayo ndipo apa ndi pomwe mayiyu anaulura m’masomuligwaa kuti ndalama yonse wakapeleka ku kachisi.

Izi zidazetsa nkangano wa ndiwe yani pakati pa a Kondwani ndi akazi awo ndipo izi zidapangitsa kuti malemuwa aganize zongochotsa moyo wake.

Thupi la malemu Kondwani linapezeka likulendewera kudenga kwa tchalitchi chomwe akazawo anakapeleka ndalama yomwe anapezayo.

Advertisement