Wachinyamata wa UTM waluma mphuno ya mtsogoleri wa MCP ku Kasungu

Advertisement
MCP member

A Alick Saini omwe amatsogolera achinyamata a UTM ku Kasungu awamanga chifukwa choluma mphuno ya yemwe amatsogolera a chinyamata a chipani cha MCP ku Kasungu komweko.

Apolisi ati nkhaniyi yachitika lachisanu usiku ku Kasunguko.

Mneneri wa a polisi ku Kasungu, a Joseph Kachikho, ati awiriwa akuti adakumana pa malo ena omwera mowa.

Ali pamalo omwewa anthuwa anayamba kumenyana ndipo mkati mwa ndewu, a Saini analuma mphuno ya wachinyamata nzawoyo yemwe dzina lake ndi Chisomo Kefa.

Apolisi amanga a Saini ndipo akuyembekezeka kupita nawo ku khoti.

Zipani za MCP ndi UTM ndi zili mu mgwirizano wa Tonse ndipo ndi zomwe zikulamula boma koma pakatipa pakhala kukokanakokana pakati pa mamembala azipanizi.

Dzulo mtsogoleri wa UTM a Saulos Chilima anati ubale wawo ndi mtsogoleri wa MCP a Lazarus Chakwera uli bwino.

Advertisement