Kwacha yagwa mphamvu

Advertisement
Wilson Banda is the governor of the Reserve Bank of Malawi which is the central bank in Malawi

Anthu m’dziko muno akuyenera kuvala dzilimbe kamba koti pali chiopsezo choti katundu wambiri atha kukwera mitengo kutsatira kuchepa mphamvu kwa ndalama ya kwacha ya dziko lino kuyelekeza ndi ndalama ya dollar ya ku America.

Lachinayi sabata ino banki yaikuluyi ya Reserve yalengeza kuti ndalama yakwacha yachepa mphanvu kuyambira lero pa 1 September, 2023.

Malingana ndi kalata yomwe tsamba lino lawona yosayinidwa ndi gavanala wa banki ya Reserve Dr Wilson Banda, ndalama ya Kwacha yagwa mphamvu ndi 2.8 kwacha pa 100 Kwacha iliyonse kuyelekeza ndi ndalama yaku America ya Dollar.

Mumchikalatachi, a Banda ati kugwa mphamvu kwa ndalama ya dziko linoku kwadziwika kutsatira msika wa ndalama zakunja omwe bankiyi idachititsa la chiwiri sabata ino pa 29 August.

Banki ya Reserve yafotokoza kuti zatelemu ndekuti ndalama ya Kwacha izigulitsidwa pamtengo wa K1,126 pa Dollar iliyonse kuchoka pa K1,095.

“Monga momwe banki ino idanenera kuyambira pa 12 January, 2023 pa malonda ogulitsa ndalama zakunja, malondawa asonyeza mtengo wa ndalama ya Kwacha moyelekeza ndi ndalama ya Dollar ya ku America (USD) ndi ndalama zina zazikulu.

“Pachifukwa ichi, chonde dziwani kuti kuyambira mawa pa 01 September, 2023, mtengo wovomelezeka wogulitsira ndalama ya Kwacha ukhala MWK1,126.77 pa USD. Chonde dziwani kuti ndalama zonse zakunja ziyenera kuyikidwa pamitengo malinga ndi malamulo a kasinthidwe ka ndalama zakunja a 2023,” yatelo banki ya Reserve.

Kutsatira kugwa mtengo kwa ndalamayi, pali chiopsezo kuti katundu ochuluka apitilira kukwera mitengo m’dziko muno zomwe zikupeleka mantha kuti anthu ochuluka omwe akuvutika kale akhala pa mavuto a dzaoneni.

Izi ndi kaamba koti ndalama ikagwa mphamvu chonchi, katundu makamaka wakunja amakhala wokwera mitengo akamalowa m’dziko muno zomwe zimapangitsaso kuti mitengo ya katundu opangidwa konkuno nayo ikwereso.

Advertisement