Khwimbi la anthu m’dera la Mangerengere Mfumu yaikulu Kapalamula m’boma la Balaka lachiwiri m’mawa lidakhamukira pa nyumba ina pomwe pagwa chinthu china chodabwitsa m’maonekedwe ndipo akukhulupilira kuti chinthucho ndi ndege ya ufiti.
Chinthu chodabwitsacho chomwe ndi lichero lomwe muli mikanda, mafupa a nyama komanso nyama yowoneka kuti yongodzongedwa kumene akuti chapezedwa panja pa chipata cha nyumbayi m’derali.
Mtolankhani wathu sadakwanitse kuyankhula ndi eni nyumba pomwe zodabwitsazi zachitikira, koma malingana ndi anthu omwe mtolankhaniyu adakwanitsa kuyankhula nawo, adafotokoza kuti usiku wapitawu eni nyumbayi adamva phokoso lochititsa mantha ndipo sakukaikira kuti chinthu chomwe chapezekachi ndi chomwe chidadzetsa phokoso la mtunduwu.
M’modzi mwa anthu omwe tidayankhula nawo, a Chimwemwe Kasambwe, omwenso amakhala pafupi ndi malo a ngoziwa adafotokoza kuti eni nyumbayi akhala akudandaula ndi za masalamusi zomwe zakhala zikuchitika pa nyumba pawo kwa nthawi yaitali.
Nawo a Phillip Bamusi ati akukhulupilira kuti zomwe zachitikazi ndi za matsenga ndipo anenetsa kuti ufiti ulipo ngakhale malamulo a dziko lino amanena kuti ufiti kulibe.
Pakadali pano, anthu adakakhamukilabe pa malopa kuti adzadyetsere maso awo pa zomwe zachitikazi.
Follow us on Twitter: