DRTSS yalanda njinga zamoto 70 zopanda chilolezo ku Zomba

Advertisement

Bungwe lomwe limawona za pamsewu la Directorate of Road Traffic and Safety Services (DRTSS) mchigawo chakum’mawa lalanda njinga zamoto 70 za anthu ochita bizinesi ya Kabanza mu mzinda wa Zomba zomwe zimayenda opanda chilolezo.

Izi bungwelo lapanga monga akunenera malamulo oyendetsera ntchito za panseu ndime 11 ndime yaying’ono yachiwiri. (Section 11 sub section 2).

M’modzi mwa akulu akulu owoona za panseu ku bungwe la DRTSS mchigawo chaku m’mawa a Moses Chisanje awuza Malawi24 kuti Bungwe lawo likulanda njingazi pofuna kuti njinga zonse zikhale zolembetsedwa.

A Masanje ati chiyambireni kulanda njingazi masabata awiri apitawa, alanda njinga 70 zosalembetsedwa ku bungwe la DRTSS ndipo iwo ati ntchito yolanda njinga ipitilira komanso achenjeza ma Kampani omwe amagulitsa njinga zamoto zosalembetsedwa mukaundula kuti ndi mulandu ndipo akapezeka adzalangidwa.

Pamenepa, iwo adakumbutsanso onse ochita bizinesi yochita njinga zakabanza kuti akhale ndi chitupa (driving license) komanso apewe kunyamula anthu opitilira awiri panjinga imodzi pofuna kupewa ngozi za panseu.

“Ife a Bungwe lomwe limawona za pamsewu tipitiliza kuphunzitsa anthu ochita bizinesi yochita njinga zamoto zakabanza momwe angamatsatire malamulo apamsewu, momwe angapezere ziphaso zapamsewu komanso momwe angalembetsere njinga zawo mukawundula wathu.” Adatero a Masanje.

Koma poyankhulapo, wapampando wa anthu ochita bizinesi yochita njinga zakabanza mu boma la Zomba a Alex Willie Kachoka adati akadokonda kuti a Bungwe la Road Traffic awapatse nthawi yoti athe kukalembetsa njingazo.

A Kachoka adatinso mdziko muno zinthu sidzikuyenda popeza posachedwa kudali matenda a Covid, Cholera komanso Namondwe wa Freddy zinthu zomwe zapangitsa kuti bizinesi isamayende bwino.

Follow us on Twitter:

Advertisement