Anthu okhala m’dera la mfumu yaikulu Kachenga m’boma la Balaka ati ndi okhumudwa ndi phungu wa nyumba ya malamulo wa m’dera la kumpoto m’boma la Balaka a Tony Ngalande ati kaamba kakuti adasiya kuwalabadira mu ntchito za chitukuko.
Poyankhulapo pakutha pa zokambilana zomwe adakonza akuluakulu a komiti yoyendetsa ntchito za chitukuko mderari (Kachenga ADC), Mfumu yaikulu Kachenga idati ndiyokhumudwa kuwona kuti ntchito zambiri za chitukuko m’derai zidaima akuti chifukwa a Ngalande adasiya kuthandizira pa chitukuko m’derari ndipo pakali pano akukhala ndi chidwi ku dera lina komwe akuwonetsa chidwi kudzapikisana nawo pa mpando wa phungu.
“Mwachitsanzo, pali zitukuko zambiri zomwe zidaima m’mbuyomu monga mlatho wa Mkasi, omwe sudathe koma ife tidauzidwa kuti ndalama zake zidatha kale,” idatero Mfumu Kachenga.
A Kachenga adawonjezelanso kunena kuti pali zitukuko zina monga kukonza chipinda chophunzilira pa sukulu ya Magomero komwe akuti zaka zitatu zapitazo kudangopita matumba a simenti makumi asanu koma mpaka pano tsogolo la ntchito yomanga chipindacho sikukudziwika.
Pothilirapo ndemanga, mkhalapampando wa komiti ya Kachenga ADC a Getrude Masten adati ndi zokhumudwitsa kuwona kuti anthu ambiri sadapindule nawo mu ndondomeko yogulitsa zipangizo za ulimi zotsika mtengo kudzera mu ndondomeko ya misika yoyendayenda yomwe akuti a Ngalande amayendetsa.
”Ndi zomvetsa chisoni chifukwa anthu a kwa Kachenga amavutika mayendedwe kupita ku Boma ku Balaka kuti akagule zipangizo za ulimi zotsika mtengo pomwe phungu wathu adangowonetsa chidwi ku madera ena ngati Khwisa komanso Matola,” adafotokoza chotero Masten.
Anthuwa akulozaso zala phunguyu ati pakuti samalongosola momveka bwino pa za kagwilitsidwe ntchito ka ndalama za mu thumba la chitukuko cha mu dera la phungu (CDF).
”Nthawi zonse tikawayitanitsa kuti atilongosolere za chitukuko cha mu thumba la CDF, iwowa samabwera ndipo izi zimatisiya ndi mtolo wa mafunso koma opanda mayankho,” adawonjezera motero Gasten.
Koma poyankhulapo, a Ngalande adati iwo akadagwirabe ntchito zosiyanasiyana za chitukuko mu derali ndipo adafotokoza kuti manong’onong’owa ndi upo chabe wa anthu ena omwe akufuna kuwayipitsira mbiri pa ndale.
”Ine ndikadali phungu wa kumpoto m’boma la Balaka ndipo ndipitiliza kuwatumikira anthu mpaka mu 2025″
”Ndikudziwa kuti pali anthu ena omwe akufuna kungoyipitsa dzina langa kaamba ka zolinga zawo pa ndale. Koma nditsindike kuti anthu a kwa Kachenga asadandaule chifukwa ine ndidakali phungu wawo,” adafotokoza chotero a Ngalande.
Iwo adawonjezeranso kuti pakadali pano sadapange chiganizo pa dera lomwe adzapikisane nawo pa zisankho za mu 2025.
Dera la Kachenga muli anthu pafupifupi 30,000.
Pa mkumanowu padalinso mafumu ena ang’onoang’ono asanu komanso nthumwi zochokera ku bungwe la NICE Trust komanso mgwilizano wa mabungwe omwe si aboma m’boma la Balaka.
Follow us on Twitter: