Tondera (kumanzere) ndi Ichocho
Mwini wake wa kampani ya Ichocho Power Security (IPS) wapepesa mtundu wa aMalawi kaamba ka kanema yomwe anajambula yolengeza kuti gulu lake lagwira ndipo likusunga mwaukapolo mkulu wa Entertainers Promotions Tonderai Banda.
Nkhaniyi inayambika lamulungu pomwe mkulu wa kampani ya IPS Yasin ‘Ichocho’ Suwedi anajambula kanema ali ndi ziphona zina za gulu lake atazungulira galimoto lina momwe akuti munali Tonderai.
Mukanemayi, Suwedi akuoneka akuuza namandwa poyimira anthu pa milandu a Jai Banda kuti mwana wawo Tonderai wagwidwa ndi gulu lawo la IPS ndipo likumusunga ngati kapolo.
Ichocho anauza a Banda kuti adzamuonaso mwana wawo Tonderai pokhapokha avomele kuyimilira gulu lake pa pempho lawo lopita ku boma kuti gululi lizitengedwa ngati gulu la asilikari a nkhondo a dziko lino.
Koma pomwe magulu ochuluka anaonetsa kusakondwa ndi zomwe zinachitikazi, Suwedi wati zomwe anayankhulazi zinali nthabwala chabe ndipo wapepesa kwa anthu onse mdziko muno omwe anakhudzidwa pa nkhaniyi.
Mkuluyu wajambula kanema ina atayima limodzi ndi Tonderai yomwe awiriwa onse akupepesa ndikupempha chikhululukiro kwa aMalawi komaso magulu ena omwe anakwiya ndi nkhaniyi.
“Ndinaona kanema wa dzulo uja (Sunday). Zimene zija sizinachitike, sanandisowetse, sichiopsezo kwa ine koma ndi onditeteza. Choncho ndikupempha kuti musamutenge ngati chiopsezo ku dziko. Zimene zija sizinali za siliyasi ndiposo ndikupepesa kuti zinachitika choncho,” watelo Tonderai.
Pophera mphongo pakupepesaku, Suwedi anati kwa anthu amene akumudziwa bwino ataona kanema oyambayo anadziwiratu kuti nkhani yomwe imakambidwa yakusowetsedwa kwa Tonderai, inali nthabwala chabe.
“Tonderai Banda sindinampange ataki (attack). Ndinatchula bambo ake chifukwa ndi mava nawo kukoma chifukwa ndi amene anali oyambilira kumandipatsa ntchito zikuluzikulu pomwe kampani yathu ya Ichocho imayamba kumene.
“Chimene chimachitika nchakuti ndikapatsidwa ntchito yoti ndigwire, nthawi zonse ndikamanyamuka pa ofesi panga kupita kumaloko, ndimajambula kanema yoti ndingoipatse moto. Koma ndivomeleze pano kuti zomwe ndinayankhulazi sizinali bwino,” wapepesa choncho Ichocho.
Iye wathokoza akuluakulu apolisi pogwira ntchito yawo bwino pankhaniyi ponena kuti anamupatsa mpata oti agwire kaye ntchito yomwe anapatsidwa paphwando la mavinidwe mumzinda wa Blantyre patsikuli kenaka ndikumufusa zonse zitatha.
Mkuluyu wati malingana ndi uphungu osiyanasiyana omwe akulandira kuchokera ku magulu a zachitetezo, azikhala osamalitsa maka kumbali ya mayankhulidwe ndipo wachenjezaso ena kuti asazapange zomwe iye anapangazi.
“Ndichenjeze ena kuti mwina mutha kuzapanga chifukwa choti ine ndinapanga. Uwu ndi mlandu ndithu moti tikuyankhula pano ndikuyenda ndichipepala cha belo (bail), tinaphwanya gawo 60 la malamulo ozengera milandu,” anaonjezera choncho Swed.
Anthu ochuluka anaonetsa kusakondwa ndi kanemayu pomwe ena ati mchitidwe ngati uwu umapeleka chiopsezo pankhani za chitetezo kaamba koti anthu amakhala ndi mantha akamayenda.
Enaso ati kupanga kanema otereyu pamene mayiko ena omwe ayandikira dziko lino ngati Mozambique kuli mchitidwe otere, ndi chibwana cha mchombo lende ponena kuti magulu ena azauchifwamba mmaiko oyanikirawa atha kutengerapo mwayi.
Follow us on Twitter: