Ophunzira wa ku UNIMA walamulidwa kukagwira ukaidi kwa miyezi 22 chifukwa chakuba

Advertisement

Bwalo la Chief Resident Magistrate ku Zomba lalamula ophunzira wa ku yunivesite ya Malawi (UNIMA) Martin Kachigayo wa zaka 26 kuti akagwire ukaidi wakalavula gaga kwa miyezi 22 chifukwa chomupeza olakwa pamulandu okuba kompyuta komanso foni.

Martin Kachigayo yemwe ndi wa mu chaka chachitatu pa yunivesite ya Malawi adaba katunduyi yemwe ndiwa ophunzira nzake wachaka choyamba  ndipo ndi wa ndalama pafupifupi 600,000 kwacha.

Martin Kachigayo adawuvomera mulanduwu ndipo adati adaba zinthuzi ndicholinga choti akagulitse kuti apeze ndalama yogulira chokudya komanso kulipilira nyumba yogona popedza alibe munthu wina aliyense yemwe amamuthandidza kumbali yamaphunziro ake.

Koma popereka chigamulo chake Chief Resident Magistrate Austin Banda adati ngakhale kuti Kachigayo kupalamula uku ndikoyamba komabe ayenera kuti alandire chilango chokagwira ukaidi wakalavula gaga kuti anthu ena atengerepo phunziro.

Chief Resident Magistrate Austin Banda adatinso akudziwa kuti ku yunivesitwe ya Malawi kuli ophunzira ambiri omwe ndi osowa koma amadzilimbikira mwa okha kuti apeze zowayeneredza zamaphunziro awo osati kuba zinthu za ophunzira anzawo.

Pamenepa Chief Resident Magistrate Austin Banda adalamula kuti Martin Kachigayo akagwire ukaidi wakalavula gaga ku ndende kwa miyezi 22 kuti anthu ena atengerepo phunziro ndipo chilangochi chidayamba kugwira ntchito kuchokera pa 19 April.

Follow us on Twitter:

Advertisement